Amayi apempha atsogoleri a ndale kuti azitukula madera awo

Advertisement
Malawi24.com

Amayi akumpoto kwa boma la Mchinji apempha anthu omwe adzapambane pampando wa ukhansala komanso phungu wanyumba ya malamulo kuti adzayambe kuganiza zotukula dera lawo m’malo moyamba kuganiza zamoyo waiwo okha.

Amayiwa anena izi ponena kuti anthu omwe amawaika pamaudindowa sayamba kuganizira anthu omwe anawaika pamaudindowa m’malo mwake amangoganiza zodzitukula iwo eni.

M’modzi wa amayiwa Chirssy Amos wam’mudzi,mwa Mpazi wati izi zinamukwiyitsa ndipo zinamupangitsa kuti asakaponye nawo voti koma anasintha maganizo kamba kabungwe loyendetsa zisankho la MEC lomwe linapita kuderali kukaphunzitsa anthu zaubwino otenga nawo mbali pachisankho..

”Ndinalimba mtima kuti sindikaponya nawo voti koma kubwera kwa bungwe la MEC lomwe linadzatiuza ubwino otenga nawo mbali poponya voti ndikomwe kunandisintha maganizo kuti ndikaponye nawo voti , koma chomwe ndingapemphe ndichoti yemwe adzapambane pachisankhochi posatengera chipani chomwe ali adzatitsitsire mtengo wafetereza, adzathetse nkhanza zomwe amayi timakumana nazo m’maanja komanso ndalama zizidzapezeka ndiwina aliense osati anthu amaudindo akulu akulu am’boma okha monga momwe zilili pano,”anatero Amos.

Pogwirizana ndizomwe mayi Amosi ananena, Mayi Lisineti Nyauleko a m’mudzi mwa Chakulamkamwa anati iwo akufuna kuti alimi azidzakhalilatu ndimisika yambewu zawo kuti akakolola asamakasowe kogulitsa komanso kuti ogulawo azidzawagula pamitengo yabwino osati mowabera.

”Ife kuno ndife alimi koma tikalima timagulidwa mbewu zathu pamitengo yotsika chonsecho fetereza timagula pamtengo okwera, chomwe ine ndikufuna ndikuti yemwe apambane pa 21 May pano adzatukule dera lathu kumbali yaulimi,komanso adzatikonzere misewu yoti tisamadzavutike potengera mbewu zathuzo kumisika,”

Ndipo m’mau ake Zione Dickson wam’mudzi mwa Mpindo wapempha anthu omwe apambane pachisankhochi kuderali kuti adzawakonzere misewu komanso masukulu adzakhale m’malo ofupikilana ndi chollinga choti ana asamadzavutike popita kusukulu zomwe zili pamitunda yaitali.

”Ife timkavutika popita kusukulu kamba kakutalika kwamitunda koma pakali pano tikupempha anthu omwe apambane pachisankhochi kuti adzaonetsetse kuti masukulu ali pafupi-pafupi kuti ana athu asadzavutikeso monga momwe ife tinkavutikila, komanso kuti misewu yopita kusukuluko idzakhale yabwino ndinso zipatala zisadzatalikilane kuti tidzapewe imfa zopeweka zomwe zimadza kamba kakutalika kwamitunda yopita kuchipatala,” anatero Dickson.

Amayiwa apereka nkhawa zawo patangotsala masiku ochepa chabe kuti dziko lino lisankhe makhansala, aphungu anyumba yamalamuro komanso  mtsogoleri wa dziko.

Advertisement