Mwana monga bambo: Atupele Muluzi azagawa mafoni 5 million akawina

Yemwe adati dzungu silibala mphonda adalinga ataona. Yemwe ndi mwana wa mtsogoleri wakale wa dziko lino a Bakili Muluzi, Atupele Muluzi wati akazawina azagawa ma lamya a m’manja komaso ma kompyuta kwa maanja zikwi zisanu (5 milliyoni).

Atupele yemwe akupikisana nawo pa mpando wa utsogoleri wadziko lino pa 21 May pano, wayankhula izi mu umodzi mwa misonkhano yake yokopa anthu.

Atupele: Azagawa ma foni

Iye wati anthu akufunika zinthu zamakono zowathandizira kupita chitsogolo komaso zomwe zingawathandizire kupanga zinthu zina mwa makono ndi mwachangu monga ma lamya za m’manja komaso ma kompiyuta.

Mtsogoleri wa United Democratic Front (UDF) yu wanena kuti banja lililonse mwa ma maanja 5 million omwe azapindule mundondomekoyi, azizawapatsa kompiyuta imodzi komaso foni imodzi yamakono.

Lonjezoli laseketsa anthu ochuluka omwe ati Atupele watengera zomwe bambo ake amalonjeza nthawi yomwe ankapangitsa misonkhano yokopa anthu pomwe ankafuna anthu kuti avoteledwe pa udindo ngati omwewu.

Anthu poyankha za lonjezoli pa tsamba la mchezo la Facebook, ati malonjezo ngati awa akungosonyeza kuti mkuluyu sanasiyane ndi bambo ake.

A Malawi afotokoza kuti kunali kwa bwino kuti anthu omwe akupikisana nawo pamaudindo osiyanasiyana azilonjeza zitukuko zosiyana siyana osati kulonjeza zinthu zomwe ndizodziwikilatu kuti sizingatheke ngati zomwe wanena Mtsogoleri wa UDF zi.

Mu nthawi yake, Bakili Muluzi analonjezapo kuti azagulira anthu m’dziko muno nsapato komaso adzamanga mlatho wapamadzi ochoka Ku Likoma kufika Ku Nkhatabay zinthu zinthu zomwe zinali nkhambakamwa chabe.

Advertisement

2 Comments

  1. His Dad promised pipo shoes..and here he comes with fones. To hell with UDF.

  2. I thought this guy was an idiot. I am not about to change my thoughts.

Comments are closed.