Ndizakumangila hotela Joyisi – Chakwera

Advertisement

Ubwenzi wa Mayi Joyisi Banda ndi abusa a Lazarus Chakwera tsopano wafika pa ndikande ndikukande. Ngakhale kuti mmbuyomu a Lazarus Chakwera ananenapo kuti Mayi Banda ndi Mfumukazi ya Mbava, pano alonjeza kuti iwo azamanga hotela akawina ndi kuitcha dzina la bwenzi wawo watsopanoyu.

Polankhula pa msonkhano omwe anachititsa pa Njamba mu mzinda wa Blantyre pamodzi ndi Mayi Banda amene analengeza kuti sapikisana nawo pofuna kupeleka sapoti kwa a Chakwera, a Chakwera analengeza kuti iwo amanga bwalo la zamesewero la tsopano mu mzinda wa Blantyre.

Chakwera ndi Joyisi

“Pano taima pano pazamangidwa stadium ya makono ndipo tizaitcha Freedom Park Stadium,” anatelo a Chakwera.

Iwo anaonjezelapo kuti pamene pali Kamuzu stadium tsopano azagumulapo ndipo azamangapo hotela ndi malo ochitilapo msonkhano zimene azazitche Dr Joyce Banda Conference Centre.

Malonjezo a bambo Chakwera akufananilanapo ndi malonjezo a bambo Peter Mutharika a chipani cha DPP.

Boma la a Mutharika lidalonjeza kuti nalo limanga stadium pa Njamba Freedom Park ndipo linatulutsa kale zifanizilo za momwe bwaloli lizaonekele. Padakali pano ku Chichiri kukumangidwa hotela.

Advertisement

2 Comments

  1. Ziliko chaka chino.manifesto amodzi mmalawi.hotelo mdzina laabandamwina mkumazawakumbukadi anthuni

Comments are closed.