Wapepesa: Ben Phiri anyazitsa DPP

Advertisement
Saulos Chilima

Woyang’anira zisankho mu chipani cholamula cha DPP a Ben Phiri apepesa ponyoza a Shanil Dzimbiri, omwe anakhalako mayi wa fuko  wa dziko lino.

A Phiri anayankhula pa msonkhano masiku apitawa kuti mtsogoleri wakale wa dziko lino a Bakili Muluzi anawasiya a Dzimbiri chifukwa choti sankagwira bwino ntchito za kuchipinda.

Saulos Chilima
Phiri: wapepesa

Mawuwa anakwiyitsa a Malawi makamaka amayi ndi a mabungwe owona za maufulu a amayi mdziko lino.

Malipoti akusonyezaso kuti mayi wa fuko a Gertrude Mutharika anaonetsaso mkwiyo atamva zomwe ananena a Phiri.

Pozindikila kuti anayankhula zoduka mutu, a Phiri apepesa kwa a Dzimbiri, amayi onse a mdziko lino komaso a Malawi onse.

“Ndikupepesa kwa Dr. Shanil Dzimbiri, banja lawo, amayi onse a ku Malawi ndi a Malawi onse omwe anakhudzidwa ndi mawu onyazitsa omwe ndinayanklhula.

“Ndikupepesaso chipani cha Democratic Progressive Party chifukwa mawu anga anayzitsa chipanichi ndipo ndikunenetsa kuti zomwe ndilankhula si maganizo a chipani cha DPP kapena mtogoleri wathu,” atero a Phiri muc chikalata chomwe atulutsa dzulo.

 

Advertisement