KFC yatsekedwa kamba ka umve

Advertisement

Imodzi mwa makampani odziwika bwino pophika zakudya zokhetsa mudyo ya KFC yatsekedwa ku Lilongwe kamba kophika zakudya mozungulira ndi zithaphwi za mphutsi, suweji ndinso nyasi zambiri za undisanzitsa.

Izi zachitika lachitatu pomwe khonsolo ya mzindawu inaona ogwira ntchito ena akumalo odyerawa akutayira nyasi mu ngalande ya nsewu wa M1 moyandikana ndi malo odyerawa pa Lilongwe City Mall.

KFC imataya nyasi mu ngalande

Malingana ndi mneneri wa khonsoloyi, Tamara Chafunya, akulu akulu amzindawu anatumiza ogwira ntchito ake kuti ayendele malo osiyanasiyana mu mzindawu.

Chafunya anati apa ndipomwe zinadziwika kuti akulu akulu a malo odyerawa sakumatsatira malamulo a khonsolo ya mzindawu pankhani yotaya nyasi ndipo analamula kuti malo odyerawa atsekedwe.

Akulu akulu amzindawa anati izi ndizopereka chiopsezo cha matenda kwa anthu omwe amapita kukadya pamalowa.

“Pa 16 April ogwira ntchito athu ena amayendera mzindawu ndipo anapeza ogwira ntchito a ku malo odyera a KFC akutaya nyasi za mchimbudzi mumngalande mphepete mwa nsewu Wa M1 olowera Ku Mbowe,” anatero Chafunya.

Mneneriyu anati akuluakulu a khonsoloyi pamodzi ndi apolisi anathamangira kumalo odyerawa ndipo kumeneko analamula kuti malowa atsekedwe ponena kuti zomwe zikuchitikazo zikupeleka chithunzi thunzi choti zinthu sizili bwino pa malo odyerawo.

Koma akuluakulu amalo odyerawa anakana kutseka malowa ponena kuti zomwe amanena akuluakulu a khonsolowa amanama koma kukanaku sikunaphule kanthu poti khonsoloyi inawapasa chikalata chotsekera malowa ndipo atsekedwa.

Padakali pano khonsoloyi yalamula kuti ngati KFC ikufuna itsegulidwe, akuluakulu a City Mall aononge malo onse osungira nyasi pamalowa.

Advertisement