Bambo anjatwa chifukwa choluma mlomo wa mwana

Advertisement

A polisi m’boma la Nkhotakota amanga bambo wa zaka 46 chifukwa chomuganizila kuti analuma mlomo wamwana wake wamamuna.

Bamboyi, Frankson Chaminju akumuganizila kuti analuma mlomo wamwana wake Chisomo Chaminju wa zaka 18 ati chifukwa chobwela pa khomo mochedwa.

Malinga ndi wachiwili kwa m’neneri wa apolisi m’boma la Nkhotakota a Paul Malimwe, bambo yemwe adali oledzela pa tsikulo, adayamba kukalipila mwana wakeyo chifukwa chomuganizila kuti adachedwa ndi anzake omwe iwo amati ndi omakhalidwe oyipa.

Mnyamatayo atakana zomwe amanena bambo akewo, iwo adayamba kumumenya paka kuluma mlomo wamwamba.

Nkhaniyi itafika ku police yaing’ono ya Mwansambo, iwo adawasaka ndikuwamanga chifukwa chovulaza mnyamatayo.

A Chaminju akuyembekezeleka kukayankha mlandu ovulaza mwana. Ndipo Chisomo akulandila thandizo la mankhwala pa chipatala cha Nkhotakota.

Bambo Chaminji, amachokela m’mudzi mwa mfumu yaikulu Mwansambo m’boma la Nkhotakota lomwelo.

Advertisement