A Katsonga akwiya ndi a Chilumpha

Advertisement

Wachiwiri kwa Mtsogoleri wa mgwirizano wa Tikonze People’s Movement a Mark Katsonga Phiri ati zomwe apanga Dr. Cassim Chilumpha popereka zikalata ku MEC ngati mtsogoleri wa mgwirizanowu mwaokha aphwanya lamulo loyendetsera mgwirizanowu ndipo iwo akadandaula ku Khoti kuti liunike nkhaniyi.

A Katsonga analakhula izi kwa mtolankhani wa MEC ku Neno lachinayi pamene amapereka zikalata zawo zofuna kupikisana nawo pa mpando wa phungu wa ku nyumba ya malamulo dera la kum’mwera kwa boma la Neno.

Malingana ndi a Katsonga, malamulo oyendesera mgwirizano wa TPM amanena kuti mtsogoleri komanso wachiwiri wake akuyenera kuvoteredwa ndi achipani osati zomwe apanga a Chilumpha zotenga wachiwiri wa mgwirizanou kunja kwa TPM.

“Izi zawonetselatu kuti a Chilumpha ndi munthu osakhulupirika. Munthu oti akukanika kutsatira malamulo a chipani angatsatire bwanji malamulo a dziko,” anatero a Katsonga.

 

Advertisement