Apolisi akwidzinga anthu atatu a bungwe la SANCO poyambitsa zipolowe pa malo a mpingo wa ECG ku South Africa

Apolisi akwidzinga anthu atatu a bungwe la Sanco amene anali mugulu loyambitsa zipolowe ndikuotcha matayala pa malo a mpingo wa ECG omwe mtsogoleri wake ndi Prophet Shepherd Bushiri mdziko la South Africa.

Apolisi amanga anthuwa atachita kafukufuku wao ndikupeza kuti gululi limachita zionetsero mosaloledwa ndi boma.

Mlembi wa bungwe la SANCO Portia Mokoena anatsimikiza za kumangidwa kwa mamembala ake. Anthuwa anamangidwa akuchoka pa malo omwera mowa mu dera la pretoria masana a tsiku lamulungu.

Chimodzi mwa zipani zandale mudziko la South Africa chotchedwa Black first Land First chatsutsana ndi mchitidwe woyambitsa zipolowe kamba ka imfa ya anthu atatu amene anamwalira mnyengo ya khrisimasi pa malo a mpingo wa ECG mu mzinda wa pretoria pamene anthu anadzetsa mdipiti ndi kupondanapondana pomwe amathawa mvula.

Chipanichi chafotokoza kuti anthu osagwirizana ndi mpingo komanso mtsogoleri wa ECG prophet shepherd Bushiri asatengere gawo pa ngozi yomwe inachitika pa malo a tchalitchiwa ndikuyambitsa zipolowe ndicholinga chofuna kubweretsa chisokonezo ndi kusokoneza bata mdziko la South Africa.

Mu chikalata chimene chinatsindikizidwa ndi mtsogoleri wa BFLF Andile Mximata, chipanichi chinamemeza apolisi kuti agwire ntchito yawo ndikuonetsetsa kuti onse amene aphwanya lamulo ndikuchita zionetsero kapena kuyambitsa zipolowe pa malo a mpingowu akwidzingidwa mopanda mantha kapena tsankho.

Zipolowe zoterezi sitinazione zikuchitika kwa mipingo ina ngakhale pali umboni osiyana siyana kuti amachita zinthu molakwika, ndikosayenera kuti tingokhala chete pamene anthu akudzetsa mpungwepungwe ndikusowetsa mtendere anthu osalakwa.

Chipani cha BLF chatsimikiza kuti anthu onse a mdziko la South Africa ali ndi ufulu wachipembedzo ndipo kuletsa gulu la anthu kusonkhana malo amodzi mu dzina lachipembedzo ndikuphwanya ufulu ngakhalenso malamulo a constitution ya dziko la South Africa.

Mchitidwe osokoneza bata ndi mtendere otere utheretu, mulekeni Prophet Shepherd Bushiri ndi anthu ampingo wake.

Advertisement