Kuli kanthu kokanthula ndichala: Chakwera ndi Chilima avulana pambalambanda

Advertisement

Pamene masiku akuthera kuchitseko kuthamangira ku chisankho chapatatu mu Meyi muno, awiri mwa anthu omwe akuzapikisana pa mpando wa mtsogoleri wa dziko atosana zala m’maso.

Lolemba sabata ino, mtsogoleri wa chipani cha United Transformation Movement (UTM) a Saulos Chilima anathira zamkamwa mtsogoleri wa chipani cha Malawi Congress Party (MCP) a Lazarus Chakwera.

A Chilima amalankhula izi pamsonkhano omwe anapangitsa pa tsikuli mumzinda wa Lilongwe ndipo anauza a Chakwera kuti asiye kuwatsata Iwo komaso asiye kuwaukira akamapanga zinthu zawo.

Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko linoyu anati a Chakwera adziwe kuti zipani zotsutsa zonse m’dziko muno sichiopsezo kutsogolo lake pa ndale ndipo anati samaopa chipani chilichose.

A Chilima anatiso mtsogoleri wa MCP yu aiwale zodzawina pazisankho chaka chino ndipo auzaso a Chakwera kuti sadzalandira ndalama za peshoni.

“Udindo wa utsogoleri wa zipani zotsutsa ulibe ndalama za peshoni. Amene ali pampando pa udindo uwu pano, adzipanga zake asamapange zaine. Asiyiletu pompano kundinyoza ine,” Anatelo Chilima.

Pozindikira kuti mamuna mzako mpachulu a Chakwera ayankha zomwe wayankhula Chilima ndipo ati iwo siokhumudwa kuti mpando wawo wautsogoleri wa zipani zotsutsa ulibe ndalama zapeshoni.
Iwo anena kuti akufuna akawina pazisankho zomwe zikubwerazi adzamange Malawi watsopano yemwe anthu onse osalandira ndalama za peshoni ngati iye mwini sazakhala akutengedwa ngati zitsilu ndi azitsogoleri awo omwe.
.
“Ndikufuna ndimange Malawi watsopano yemwe anthu zikwizikwi omwe simulandira ndalama za paeshoni simudzidzaonedwa ngati zitsiru komaso Malawi yemwe nonse amene mumatumiza ana anu ku masukulu aboma simudzidzakanizidwa mwayi wa ntchito omwe pano ukumapelekedwa kwa ana amabwana omwe akumaphuzira sukulu za pamwamba,” anayankha choncho Chakwera.

Chakwera anaonjezera kunena kuti iye ndimunthu wa Mulungu yemwe samakakamira ma ofesi aboma ndicholinga chofuna kumazithandiza okha monga akupangira a Chilima pokana kutula pansi udindo wa wachiwiri wa mtsogoleri wadziko

Iwo anatiso Chilima akuyenera kutula pansi udindo wake kamba koti sakugwira ntchito ndipo wapempha anthu onse mdziko muno kuti amuvotere pazisankhozi ponena kuti iye sakufuna mpandowu ndicholinga chofuna kuzithandiza yekha.

“Kumapeto kwake tizakhala ndi mtsogoleri yemwe chidwi chake ndi inu nonse pamodzi ndi mabanja anu ndipo tonse tizayamba kuchita bwino limodzi ndipo sipazakhala kunyoza anthu omwe samalandira ndalama za peshoni,” anaonjezera choncho Chakwera.

Advertisement

One Comment

  1. The only problem is that MCP will NEVER EVER win the elections that’s the only problem. They’re ok as opposition with a leader of of opposition trying hard to get a job that will guarantee him pension yet the Vice President who has got pension even if he chooses to retire active politics will be looking to serve Malawians. So MCP the souls of those forced to depart the likes of Muwalo, Matenje, God amazing etc etc are still crying kuli Chester so there is no chance.

Comments are closed.