Sindinamvetse bwino malamulo – watero ofuna uphungu

Advertisement

A Hebrews Misomali omwe amagwira ntchito ku ofesi ya mtsogoleri wa dziko lino asintha chiganizo chopikisana nawo pa zisankho za aphungu ku Neno boma litawauza kuti akuyenera kusiya ntchito m’boma.

A Misomali amafuna apikisane nawo pa zisankho zofuna kupeza odzaimira chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) pa zisankho za aphungu ku dera la kumpoto kwa boma la Neno.

Iwo auza mtolankhani wa MEC ku Neno lachiwiri kuti atakambisana ndi mabwana awo pa za malamulo omwe amayenera kusata ngati kufuna kuyamba ndale posakha chimodzi pakati pa  ndale ndi tchito, iwo ati asankha zopitiliza kugwira ntchito m’boma ndi kulengeza kuti saimaso ngati phungu ku mpoto kwa boma la Neno.

Iwo anati ataunguza mbali ziwirizi anachiona cha nzeru kuti azasiye ntchito m’boma ndi kuzapitiriza khumbo lawo lofuna kukhala phungu wa ku nyumba ya Malamulo chaka cha 2024.

Padakali pano a Misomali akugwira ntchito ku offesi ya mtsogoleri wa dziko lino ku nthambi yoona za uchembere wabwino ngati Resource Mobilization Director.

“Uthenga wanga kwa onse ondisatira ndioti asataye chiyembekezo ndikhala ndikubweranso 2024. Ndikudziwa tinatha kale mtunda, ndipo ena sachilandira bwino chinthuchi koma ndinayenera kupanga chiganizo chabwino popangira pa mawa,” anatero a Misomali.

Atafunsidwa ngati nthawi yonseyi samadziwa za malamulowa, a Misomali anati amadziwa zoti munthu amayenera kupuma pa ntchito kuti alowe ndale koma sanamasulilidwe bwino za malamulowa kufikira pomwe mabwana awo anawaunikira ndondomeko yonse yomwe imasatidwa munthu akafuna kusiya ntchito mwa njira imeneyi.

Komabe a Misomali anati athandizana ndi amene apambane pa zisankho za chipulura ku chipani cha DPP chomwe chizapangitse zisakhozi pa 23 December ku dera la kumpoto kwa Neno komwe iwo amafuna kuimira.

”Mukandifunsa kuti ndithandiza ndani pa makandideti omwe akuimira ku Neno, ine ndizagwira ntchito ndi amene apambane pa chisankho cha chipulura ku DPP, koma nkhawa yanga ndiyoti phungu yemwe alipo panoyi walephera ntchito yake, palibe cholozeka chomwe wapanga. Koma ine ndizasitha izi mu 2024,” anatero a Misomali.

Kusatira izi, zikutanathauza kuti anthu awiri  omwe ndi phungu wa derali a Emmnuel Lonzo ndi Thoko Tembo yemwe ndi mwana wa kadaulo pa nkhani zoulutsa mau  Benson Tembo ndi amene apikisane pa zisakho za chipulura za DPP ku dera la kumpoto kwa boma la Neno.

Ndipo yemwe azawine pa zisakho za chipulura ku DPP azapikisana kwambiri ndi woimira chipani cha People’s a Osteen Gunde komanso katswiri pa nkhani za ufulu wa anthu ndi ulamuliro wabwino a Odreck Kathamalo omwe asiya ntchito ku bungwe lophuzitsa anthu za chisankho la NEST ngati mkulu owona za mapulogalamu ku bungweli.

Advertisement