Zambia yatenga mbali ina ya Malawi


Jean Kalilani

A Malawi ena omwe amakhala mmalire mwadziko lino ndi Zambia apezeka ali m’dziko la Zambia kutsatira kudulaso malire pakati pa maiko awiriwa.

Izi zikutsatira kulengeza komwe boma la Malawi lapanga kunena kuti mbali ina yomwe mwini wake linali dziko lino si ya Malawi koma ndi ya Zambia.

Malingana ndi nduna ya dziko lino yoona za malo, nyumba ndi chitukuko cha m’matauni a Jean Kalilani, kudulaso kwa malilewa kwakhudza mbali zina m’maboma monga Mchinji, Mzimba, Kasungu komasi boma la Rumphi.

A Kalilani amayankhula izi ku nyumba ya malamulo pomwe anapatsidwa mwayi oyankhula ngati nduna.

Iwo anena kuti ma boma awiliwa agwirizana kuti anthuwa azikhala kaye malo omwewa kufikira maikowa atagwilizana chinthu chimodzi chenicheni choyenera kuchitika pa anthuwa.

“Maiko awiriwa posachedwa pomwepa akhala akugwirizana choyenera kuchita akamaliza onse kulandira malipoti okhudza nkhaniyi.

“Choncho ndikupempha anthu onse okhudzidwa ndi nkhaniyi kuti apitililebe kukhala mzika za kuMalawi kuno ndipo ali ololedwa kulembedwa ndi atsogoleri a m’madera mwawo kutsimikizika kwankhaniyi kukachitika masiku akubwerawa,” watero Kalilani.

A Kalilani achondelera a Malawi omwe amakhala m’maliremu kuti asasinthe umzika wawo ndipo apempha kuti iwo apitililebe kukhala mzika za dziko lino.

Nkhani yokhudza kusintha malire a pakati pa dziko lino ndi Zambia linayamba muchaka cha 1993 ndipo akuluakulu a maiko awiriwa akhala akuchita kafukufuku okhudza malilewa kuyambila mchakachi kufika pano pomwe zadziwika kuti malo omwe anali mmanja mwa Malawi eni ake ndi a dziko la Zambia.

2 thoughts on “Zambia yatenga mbali ina ya Malawi

Comments are closed.

Discover more from Malawi 24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading