Chilima zamvuta, atha osaima 2019

Advertisement
Saulos Chilima

….tikamangala, yatero UTM

Pali chiopsezo choti wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino a Saulos Chilima atha osapikisana nawo paudindo wa mtsogoleri wa dziko lino pa chisankho cha patatu chomwe chitachitike chaka mawa chino.

Chilima: UTM yakanidwa

Izi zikutsatira kukanizidwa kulembetsa gulu lawo landale la United Transformation Movement (UTM) lomwe a Chilima akuenera kuzaimila ngati mtsogoleri pa zisankho zikubwerazi.

Malingana ndichikalata chomwe anatikitira ndi wachiwiri kwa mkulu owona zolembetsa zipani zandale (Registrar of Political Parties in Malawi), a Chikumbutso Namelo, iwo akana kulemba gulu landale la UTM mkaundula kamba koti pali zinthu zina zomwe zikutsutsana ndi malamulo olembetsera zipani.

Mumkalatamu a Namelo anena kuti ndizosatheka kuti chipanichi chilembetsedwe mumkaundula wawo ndi dzina loti UTM pamene chikudziwika komaso kuchita zinthu zake mu dzina loti United Transformation Movement osati UTM.

Iwo afotokoza kuti izi ndizosaloledwa mu mmalamulo olembetsera zipani ndipo ati sizingatheke kulemba chipanichi mkaundula.

“Ndicholinga chofuna kulembetsa chipanichi, akuluakulu a UTM mwadaladala anapeleka makalata awo olembetsera omwe sakuonetsa mboni pa dzina lawo lomwe akhala akudziwa nalo” Yatelo Mbali Ina ya kalatayo.

Iwo apitiliza ndikuopseza chipani cha UTM kuti ndikulakwila malamulo awo kupeleka uthenga wolakwika okhudza chipani chawo

Kupomboneza mkulu wo lembetsa zipani zandale ndicholinga choti chipani chanu chilembedwe munkaundula wazipano ndimulandu ndipo ndikuphwanya malamulo. Choncho ndakana kulemba chipani cha UTM mumkaundula Wa zipani” watelo Namelo.

Poyankhapo pakukanizidwaku gulu la ndale la UTM latsutsa maganizo ankuluyu ndipo chafotokoza kuti chitengera nkhaniyi kubwalo lalikulu LA milandu.

Oyankhulira chipani cha UTM a Joseph Chidanti Malunga ati ndiokhumudwa ndinkhaniyi makamakaso kuti a Namelo sanawapatse mwayi oti amve mbali yawo.

“Ife tikutsutsa mwantuu wagalu maganizo omwe mkulu ameneyu akunena pazifukwa zingapo? Watelo Malunga munkalata.

Gulu la UTM likutsogoleledwa ndi a Chilima omwe ananena za chidwi chawo chopikisana pa mpando wa mtsogoleri wadziko madzi atachita katondo Ku chipani cha DPP.

Advertisement

3 Comments

Comments are closed.