Mgwirizano ndi DPP: Ndi nkhambakamwa chabe – yatero UDF

Atupele Muluzi, Peter Mutharika

Chipani cha United Democratic Front (UDF) chanenetsa kuti sichinapange ganizo logwira ntchito ndi cholamula cha Democratic Progressive Party (DPP) pa chisankho cha 2019.

Mneneri wa chipani cha UDF a Ken Ndanga ndi yemwe wanena izi poyankhulapo pa malipoti omwe akumveka akuti mtsogoleri wa dziko lino a Peter Mutharika akulingalira zozasankha a Atupele Muluzi ngat wachiwiri wawo pa nthawi ya zisankho za pulezidenti chaka cha mawa.

A Ndanga anati padakali pano chipani chawo sichili pa mgwirizano ndi chipani chilichonse.

Koma anapitiliza kunena kuti mwayi ulipo oti chipani cha UDF chitha kupanga mgwirizano ndi chipani china.

“UDF ikaganiza zogwira ntchito ndi chipani china chirichonse pa chisankho cha 2019 sidzidzakhala zobisa.

“Nkhani ngati iyi imafunika kulingalira modekha ndikuganizira kwambiri zofuna anthu.

“UDF idzalengeza poyera ngati izi zidzachitike. Pakali pano palibe chirichonse,” anatero a Ndanga pa tsamba lamchezo la Fesibuku.

Kumayambiliro a mwezi uno mtsogoleri wa UDF Atupele Muluzi anamusankha ngati ozayimilira chipanichi pa chisankho cha pulezidenti zomwe zichitike chaka mawa.

Koma zikumveka kuti a Muluzi omweso ndi nduna ya za umoyo atha kusankhidwa ngati wachiwiri wa a Mutharika pa masankhowo.

Advertisement