Mbalame ibwelera kuchitsa: Chimunthu akubwelera ku DPP, ati akukamuchotsapo Chilima

Advertisement
DPP

Pamene zikuoneka ngati namtindi wa anthu ukulongeza atatede awo ndi kumaliyasa la mtondo wadooka kulowela ku chipani chatsopano cha UTM, sipikala wakale wa nyumba ya malamulo a Chimunthu Banda akulowela Kwinako.

Malinga ndi malipoti, Mtsogoleri wa chipani cholamula cha DPP a Peter Mutharika akuyembekezeka kulandila mu chipani a Chimunthu Banda amene pakatipa analengeza kuti asiya ndale.

Chimunthu Banda ali ku DPP kachikena.

A Chimunthu Banda mmbuyomu anapikisanapo ndi a Peter Mutharika pa utsogoleri wa chipani cha DPP koma anagwa chagada. Iwo kenako analengeza kuti tsopano apuma pa ndale.

Koma pang’ono pang’ono anayamba kuonekanso ku misonkhano ya chipani cha DPP kupangitsa anthu kunena kuti a Chimunthu abwelera ku ndale.

Malipoti anazamvekanso kuti a Chimunthu akufuna udindo wa mlembi wamkulu wa chipani omwe pakali pano uli ndi a Grezelder Jeffrey koma zinaoneka kuti si zoona.

Ena akuti pa chisankho cha 2019, a Chimunthu aima ndi a Peter Mutharika.

Advertisement

One Comment

  1. Atleast we need Chimunthu for runningmate not this snake Atupele Muluzi. Dont give power back to the Muluzi family.

    DPP4Life

Comments are closed.