Mutharika: Chilima wabodza

National

Ntchito 1 miliyoni pa chaka? Haha ndi bodza la nkhukuniza – Mutharika

By Malawi24 Reporter

August 09, 2018

Wandisokosela n’kulinga utamva, ndipo chulukechuluke ngwa njuchi yomwe umanena iwe ndi yomwe yakuluma.

Mutharika: Chilima wabodza

Mtsogoleri wa dziko lino a Peter Mutharika wati zomwe akunena wachiwiri wawo a Saulos Chilima zoti pasanathe chaka azakhala atapanga ntchito 1 miliyoni ndi zabodza.

Malinga ndi uthenga ofuna kuutsa mudyo a Malawi kuti amvele ndi kuonela pologalamu imene a MBC akhale akucheza ndi a Mutharika, a Mutharika akunena kuti ndi nthabwala zoti munthu atha kukhazikitsa ntchito 1 miliyoni ku Malawi kuno.

A Chilima anasiyana ndi a Mutharika ndi kukayambitsa chipani chawo atalephera kuchotsa a Mutharika pa udindo otsogolera chipani cha DPP. Pokhazikitsa chipani chawo, a Chilima anauza a Malawi kuti akawasankha iwo azapanga ntchito 1 miliyoni kuti a Malawi osowa ntchito apeze pogwila mu miyezi isanu ndi umodzi yokha.