Malawi 24

Zotukwanizana sizabwino – Atcheya

Ati ndale kumapanga koma mwaulemu. Osati mukafika pa nsanja koma ndiye kutukwana. Atcheya Bakili Muluzi ati zimenezo ayi.

Mtsogoleri opuma a Bakili Muluzi adzudzulidwa ndi kuyamikilidwa pa nthawi imodzi kamba kodzudzula atsogoleri a ndale chifukwa chokonda zonyozana.

A Muluzi kufika pa mtsokhano waukulu wa chipani cha UDF.

A Muluzi amene ulamuliro wawo unachuluka ndi kunyozana ndipo iwo anadziwika ndi kutha kunyoza anauza nthumwi ku msonkhano waukulu wachipani cha UDF kuti ndale tsopano zakalaluka.

“Munthu sungamanene Mtsogoleri wa dziko kuti mtchona olo zitavuta motani,” anatelo a Muluzi podzudzula maka Mayi Callista Mutharika amene akumanyoza a Peter Mutharika pa misonkhano ya chipani cha UTM.

Koma ena ati a Muluzi si munthu oyenela kulankhulapo pa nkhaniyi kamba koti iwo ndiwo anabweletsa ndale zonyozana mu dziko muno.