Zotukwanizana sizabwino – Atcheya

Advertisement
UDF

Ati ndale kumapanga koma mwaulemu. Osati mukafika pa nsanja koma ndiye kutukwana. Atcheya Bakili Muluzi ati zimenezo ayi.

Mtsogoleri opuma a Bakili Muluzi adzudzulidwa ndi kuyamikilidwa pa nthawi imodzi kamba kodzudzula atsogoleri a ndale chifukwa chokonda zonyozana.

UDF
A Muluzi kufika pa mtsokhano waukulu wa chipani cha UDF.

A Muluzi amene ulamuliro wawo unachuluka ndi kunyozana ndipo iwo anadziwika ndi kutha kunyoza anauza nthumwi ku msonkhano waukulu wachipani cha UDF kuti ndale tsopano zakalaluka.

“Munthu sungamanene Mtsogoleri wa dziko kuti mtchona olo zitavuta motani,” anatelo a Muluzi podzudzula maka Mayi Callista Mutharika amene akumanyoza a Peter Mutharika pa misonkhano ya chipani cha UTM.

Koma ena ati a Muluzi si munthu oyenela kulankhulapo pa nkhaniyi kamba koti iwo ndiwo anabweletsa ndale zonyozana mu dziko muno.

Advertisement

9 Comments

  1. He is the one who laid a very bad foundation of democracy in this nation. Muluzi is to blame for everything bad happening in malawi. Let him not say anything, and that is why Atupele can not achieve anything politically because he is paying for the sins of his father.

  2. Hahahahaa zinanalakwika pachiyambi..munayamba ndinu.. Nato tiyanat tinayamwila

  3. Atcheya musandiseketse mwava. M’dya makoko saiwala. Inu ndiye kuchitekete ko nyoza azanu. Munazidzala izi nokha

  4. Bakili apepese Kaye Ku mtundu wa a Malawi popeza iyeyo anayambitsa ndale zonyozana mu ulamuliro wake

  5. Iwo aiwala kuti kutukwana anatiphinzitsa okha.anamutukwana Malewezi Chakuamba Mpinganjira.Akuona ngati tayiwala?

Comments are closed.