Tapita ife – Kongeresi ndi PP anyanyala pa mkumano ndi MEC

Chakwera

Zipani zotsutsa za Kongeresi ndi PP zinagwilizana zonyanyala mkumano okumana ndi a MEC pamene amafuna kumvana pa nkhani ya mmene kalembera wa anthu ovota akuyendela.

Pa mkumanowu, nduna yofalitsa nkhani a Nicolas Dausi inapempha a MEC kuti asamvele zimene akunena a Zipani zotsutsa kuti iwo achititsenso kalembera ku madera amene anthu ochuluka sanatuluke kukalembetsa.

Dausi
A Dausi inapempha a MEC kuti asamvele zimene akunena a Zipani zotsutsa

A Dausi ananena kuti silinali vuto la MEC kuti anthu analephera kukalembetsa, iwo anati a Zipani ndiwo analephera kumema anthu kuti akalembetse.

Koma nkhaniyi inakwiyitsa anthu a zipani zotsutsa amene akufunitsitsa kuti kalembera wa anthu ovota achititsenso ku madera amene anthu anatuluka ochepa.

Zitaoneka kuti nkhaniyi yamela matewe ndipo ilibe tsogolo, mlembi wamkulu wa chipani cha Kongeresi a Eisenhower Mkaka pamodzi ndi a Ibrahim Matola a PP ananyanyalapo basi ndi kutuluka mu zokambilanazo.

Advertisement