Zopatsa chidwi: Bambo apangitsa mwambo otsekulira chimbudzi

Lilongwe
Lilongwe
Mwambo otsegulira chimbudzi cha bambo Finyani.

Yemwe adanena mwambi oti zina ukamva kamba anga mwala adalinga ataona ndipo adadziwa kuti china chake chosachitikachitika chizachitika mumzinda wa Lilongwe kuti mwambiwu udzagwire ntchito lero.

Mu nkhani yopatsa chidwi ndikulingalilitsa kuti opangayo anaganiza motani, njonda ina ku Lilongwe m’mudzi wa a Sankhani mfumu yaikulu Njewa inapangitsa mwambo otsekulira chimbudzi.

Mwini wake malo odzithandizilawa omwe ndibambo Finyani adaitanitsa mwambo otsekulira chimbudzichi lachisanu lapitali pa 6 Julaye.

Pomwe anthu anali atasonkhana Ku Mzuzu pa chisangalaro kuti dziko lino lakwanitsa zaka makumi asanu ndi mphambu zinayi (54) lili pa ufulu odzilamulira lokha, naye mkuluyu anali atasonkhanitsa anthu kuzaonelera mwambo otsekulira kanyumba kake kozithandizira m’mimba mukatentha.

Chinthu china chopatsa kaso pa nkhaniyi ndichakuti mkuluyu mpaka anafika poitana mulendo olemekezeka pamwambowu omwe anali bambo Makupete omwe ndi m’modzi mwa anthu okhupuka m’delari.

Zithunzi zina zomwe nyuzipepala ino yazipeza zikuonetsa bambo Finyani ataima ndi akazawo kwinaku akumanga lamba wa buluku lawo panja pa chimbudzi chomwe chimatsekulilidwacho­­, chisonyezo kuti mwambowo wathekadi.

Mwezi wa May nkhani inali ponseponse pa tsamba lamchezo la fesibuku pomwe anthu amdziko la Zambia anaseka chihehede pa nkhani yomwe inamveka yoti mtsogoleri a dziko lino a Peter Mutharika nawoso anatsekulirako chimbudzi.

LilongweChinatsitsa dzaye kuti njobvu ithyoke mnyanga mchakuti a Mutharika anajambulidwa akusonyezedwa zinthu zomwe ana asukulu ya ukachenjede a pa Namilonga Community Technical Colleges amapanga.

Pachithuzipa a Mutharika anali akusonyezedwe chimbudzi chamakono chomwe chinapangidwa ndi ophunzilawa koma izi sizinali chimodzimodzi ndi anthu aku Zambiawa.

Iwo munkuona kwawo pa chithuzi chomwe sichidasiye malo ankaona ngati a Mutharika anali akutsekulira nyumba yodzithandizirayi ndipo anaseka chiphwete chofa nacho kwinaku akumutafunira lilime mtsogoleriyu kuti wasowa chochita.

Advertisement

4 Comments

  1. KKKKKKKKK, Chamba chikulimidwa ku Nkhotakota, koma ofoira amakhala anthu akutali ndi Nkhotakota ngati amenewa. If not weed then this guy is mad

Comments are closed.