Boma la Karonga lipindula zedi ndi bajeti, atero Mwenifumbo

Advertisement
AFORD Mwenifumbo

Phungu waku nyumba ya malamulo m’dera la pakati m’boma la Karonga a Frank Tumpale Mwenifumbo, wayamikira msonkhano wa a phungu omwe wangotha kumene kunyumba ya malamulo mu mzinda wa Lilongwe omwe aphungu amakakambirana ndondomeko yaza chuma cha dziko lin-o cha zaka za 2018 mpaka 2019 ponena kuti dera lawo lipindula kwambiri ndi ndondomekoyi.

A Mwenifumbo omwe ndi a Alliance for Democracy (AFORD) analankhula izi pa msonkhano wa atolankhani omwe anachititsa pa Mikoma m’dera lawo omwe cholinga chake kunali kuwuza anthu a ‘mdera lawo zomwe akatenga ku msonkhano wa a phunguwa.

AFORD Mwenifumbo
Mwenifumbo: Msonkhano wa a phungu wayenda bwino.

Iwo adati mwa zina, aphunguwa akambirana malamulo angapo ndipo limodzi mwa malamulowa ndi lokhudza ndalama zankhani-nkhani lomwe likudikira President wa dziko lino Arthur Peter Mutharika kuti alivomereze.

A Mwenifumbo adati lamulo limeneli lipereka mphamvu ku boma kukongola ndalama zaku Amerika zokwana 26 million kuchokera ku banki ya chitukuko yaku Africa zomwe zigwire ntchito yobweretsa madzi akumwa aukhondo m’boma la Karonga.

“Paja madzi ndi moyo, choncho mwachidule ndinene kuti ndalama zankhaninkhani zimenezi zibweretsa moyo kumadera akumidzi monga Katili, Mwenilondo, Lupembe, Mlare, Lugali komanso Kasimba komwe kwa nthawi yayitali anthu akhala akumwa madzi osatetezeka,” iwo adatero.

“Powonjezera apo, ntchitoyi ikayamba, achinyamata ambiri m’dera langa komanso boma la Karonga adzapeza mwayi wa ntchito,” anaonjezera motero a Mwenifumbo.

M’mawu awo iwo adati boma layikanso ndalama zina zankhaninkhani zomwe zigwire ntchito yaikulu ya ulimi wa mthilira m’derali ngati njira imodzi yochepetsera mavuto a kuchepa kwa chakudya m’boma la Karonga.

“Dera la pakati la boma lino la Karonga limalandira mvula yochepa zedi pa chaka kotero kuti anthu sakolola chakudya chokwanira. Choncho ntchito ya ulimi othilira idzathandiza anthu kulima mbewu zosiyanasiyana, zina zakudya komanso zina zogulitsa,” iwo adatero.

A Mwenifumbo adayamikira anthu a m’dera lawo chifukwa cholimbikira pa nkhani ya chitukuko. Iwo adapereka chitsanzo cha chipatala cha Mwenilondo chomwe anthuwa amanga ndi ndalama zawo. Iwo adatsimikizira anthuwa kuti boma lagula kale makina a pamwamba, mabedi, mipando ndi katundu wina wambiri wapa chipatalapa.

Atafunsidwa ngati chipani cha AFORD chili ndi maganizo olowa mu mgwirizano ndi zipani zina pa chisankho chapatatu cha mchaka cha 2019, iwo adati nthawi yakwana yoti zipani zina zipemphe chipani chawo za mgwirizano chifukwa chipani cha AFORD chakhala chikuthandiza zipani zina m’mbuyomu pa chisankho.

“Ine ngati mtsogoleri wa chipani cha AFORD, ntchito yanga yaikulu ndi kudzutsanso chipanichi kuyambira ku Karonga kuno mpaka ku Nsanje, Mchinji mpaka Mangochi. Ndi zomvetsa chisoni kuti mchaka cha 1994 chipanichi chinali ndi aphungu 26 kunyumba ya malamulo ndipo padakali pano chili ndi phungu m’modzi yekha basi,” adatero a Mwenifumbo.

Iwo adatsindika kuti anthu akadzawasankha kukhala mtsogoleri wa dziko, boma lawo lidzapereka mphamvu kuwanthu ngati njira imodzi yopereka umwini ku chitukuko cha dziko zomwenso zidzachepetse mchitidwe wa katangale ndi ziphuphu.

Malinga ndi a Mwenifumbo, dziko la Malawi litha kutukuka ngati anthu atayika m’mipando anthu amene alibe khalidwe la dyera komanso atsogoleri okhawo amene amakonda dziko lawo ndi mtima onse.

“Anthu adzisankha atsogoleri okhawo amene ali ndi chidwi ndi ntchito za chitukuko, atsogoleri opanda tsankho, opanda dyera komanso osapanga zinthu mobisa. Mtsogoleri adzikhala wa ntchito wa anthu a kumudzi, mtsogoleri asamakhale bwana kapena dona,” adatero a Mwenifumbo
Pa msonkhanowo, a Mwenifumbo anati chisankho cha 2019 chikhala chomaliza kuyima ngati phungu wa dera lapati m’boma la Karonga. Iwo adati ali ndi chikhulupiliro kuti pa nthawiyi adzakhala atamaliza ntchito za chitukuko zomwe anakonzera anthu a m’derali.

Advertisement