Khala chete ndi mbwelera zakozo – akatswiri auza Chakwera

Advertisement
Lazarus Chakwera

Akanakhala a Chilima ndi mikuluwiko yawo ija, mwina akanati n’konzen’konze ananyula maliro a eni; kapena akanangojama mulomowu ya Ma Blacks.

Mkulu wa zipani zotsutsa boma mu nyumba ya malamulo amenenso ndi Mtsogoleri wa chipani chotsutsa cha Kongeresi wadzudzulidwa kolimba pa ganizo lake loti a Mutharika aitanitse zisankho zatsopano.

Lazarus Chakwera
Katswiri wazamalamulo wati a Chakwera ndi adyera.

A Chakwera adanena izi pothililapo ndemanga pa nkhani yoti a Mutharika akuganizilidwa zopindula ku ndalama zakuba.

Pothililapo ndemanga pa nkhaniyi a Chakwera anati a Mutharika angoyenela kutula pansi udindo pamodzi ndi boma lawo lonse. Iwo anatinso a Mutharika aitanitse chisankho cha mmangummangu.

Koma akatswiri azamalamulo ndi ena andale ati ndemanga ya a Chakwera ndi yolakwika ndi yongotsogozedwa ndi dyera.

Iwo ati malinga ndi malamulo a dziko lino, palibe chifukwa choti wina akambe za chisankho cha madulira.

Malinga ndi akatswiriwo ati malamulo akunena moona mtima kuti ngati Mtsogoleri watula pansi udindo, wachiwiri wake akuyenela kutenga.

Iwo ati ngati a Mutharika angatule pansi udindo kapena kuchotsedwa, a Saulos Chilima aiphula basi.

Advertisement

8 Comments

  1. Kuzolowera kuba basi.cashgators. Nothing wrong Dr Chakwera said. 2019 muonaso

  2. Zisankho ndi 2019 basi, palibe madulira.ife pambuyo pa DPP ndi APM

  3. A presidential aspirant who doesn’t know/understand the laws of the country. How is he going to rule?

  4. Amene mwalemba nkhaniyi mukungoonetsa kuti mumadana ndi a Chakwera, but that is not proffessional journalism. Thats not the way you should have presented this issue. Akukutuman eti? Umphawi ndi khwinthi la ndalama zikupweteketsani

  5. Zoona izi, mkuluyi ndiwadyera, osakhazikika maganizo, ofunisitsa udindo… Mukumbuke 2014 elections

  6. Your primitive web is out of synchronization with the current state of affairs, foolish..!!! …what wrong has Chakwera done… thieves must go…and they must goo!!!

  7. kkkkkkk monga inu mukuonapo chodabwitsa? A chakweratu anazolowela zitsankho zamadulira, kumbukilani conversion yao, pajansotu inali yamadulira. Tikunenetsa ife kuti chakwera ngwadyera ndipo sakuyenera kulamulira dzikoli.

Comments are closed.