Chaponda wazisiyanso!!

Advertisement
George Chaponda

Adayamba ndi wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino a Saulos Chilima kuimika manja kuti sakufuna kupikisana nawo pa udindo ulionse m’chipani cholamula cha Democratic Progressive Party (DPP) ku msokhano wake waukulu.

Mauwa anabwerezedwa ndi yemwe anali wachiwiri kwa mtsogoleri m’chipanichi a George Chaponda omwe dzulo anayimika manja kuti sapikisana nawo pa mpando wa wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipanichi kum’mwera.

George Chaponda
A Chaponda anakana kupikisana nawo pa mpando wa wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipani cha DPP kum’mwera.

Yemwe akuyendesa mwambo wa mkumano wachipani cha DPP a Nicholas Dausi anauza khwimbi la anthu lomwe lasonkhana mu mzinda wa Blantyre kuti a Chaponda aganiza zoti asapikisane nawo pa mpando wa wachiwiri kwa mtsogoleri m’chipanichi.

A Dausi anasindika kuti a Chaponda apeleka ganizoli pa zifukwa zao, zomwe sadazinene.

Pomwe a Dausi amapeleka uthengawu ku holo la Comesa lolemba, otsatira chipani cha DPP ena anawombela m’manja uku malikhwelu akuombedwa ndi chimwemwe.

Ganizo la a Chaponda linachepetsa omwe nambala ya omwe amapikisana pa mpandowu kuchoka pa anayi kufika pa atatu.

A Kondwani Nankhumwa, a Joseph Mwanamveka ndi a Henry Mussa ndi omwe anapindilana ndebvu mkamwa kufuna mpandowu.

Advertisement