‘Titchipitsileni’: ung’onoung’ono ukufuna mtengo opikisana pa chisankho awasitsile

Charles kajoloweka

Zikamatha zisankho za 2019, a mabungwe akufuna achinyamata azakhale adzadza mu ma udindo ovoteledwa.

Koma malinga ndi amabungwe amene asonkhana pamodzi kuti aonetsetse kuti achinyamata agwetsa madala mu zisankho, bungwe loona za zisankho la MEC likuyenela kufewetsa ka mtengo pang’ono ndi cholinga achinyamata ochuluka akwanitse kupikisana nawo pa chisankho.

Charles kajoloweka
Kajoloweka: Zinthu zikuyenela kusintha.

Malinga ndi mkulu otsogolera ma bungwe amenewa, a Charles Kajoloweka, ati mitengo imene ayika pano ndi yokhwima kwa achinyamata ambiri.

“Achinyamata ndi ochuluka koma mukaonetsetsa mu ma udindo ambiri munachuluka anthu akulu akulu, zinthu zikuyenela kusintha,” anatelo a Kajoloweka.

Iwo anaonjezelapo kuti njira imodzi yosinthila zinthu ndi kuonetsetsa kuti mtengo oti achinyamata azilipila kuti apikisane nawo utsitsidwe ndi theka. Anati izi zithandiza maka achinyamata akumidzi kuti akwanitse kupikisana nawo pa zisankho.

Bungwe la MEC lati iwo amakhala ndi nthawi yokumana ndi mabungwe ndi anthu okhudzidwa ndi zisankho ndipo nkhaniyi ikazayambitsidwa kumeneko azatha kuiganizila.

Pa chisankho cha 2014, opikisana onse achikazi anapeleka ndalama yochepelapo kusiyana ndi anzawo achimuna.

Advertisement