A Chilima akulingalila zothawa mu DPP

Pamene mbali inayi anthu akuti mkuluyi ndi Abisalomu ofuna kulanda ufumu wa Bambo ake, kwinaku ena akuombela m’manja mkuluyi kuti iye yekha ndiye ali ndi kuthekela kophula DPP, wachiwiri kwa Mtsogoleri wa dziko lino a Saulos Chilima aulula kuti iwo atha kuchithawa chipani cha DPP.

Saulos Chilima
Chilima: Akuganiza zotuluka DPP

Polankhula pa mwambo wa mpingo wa katolika, a Chilima anati mu boma anthu akuba mochititsa manyazi komanso mopanda chikondi.

“Sizikuwakhudza kuti akubela anthu osauka. Anthu akuzunzika chifukwa cha kuba, odwala akufa m’zipatalamu,” anatelo a Chilima.

Iwo anati mmene anthu akubela, ndi zinthu zopangitsa band ‘kugawana zida’.

Izi zatanthauzilidwa kuti a Chilima ali ndi chilinganizo choti achoke mu chipani cholamula cha DPP ndi kukapanga zawo paokha.

Koma anthu ena ati makhalidwe a Chilima ndi autambwali kamba koti iwo akhala ali m’boma lomwelo kwa zaka zonsezi.

Advertisement

One Comment

  1. Ndikoyenela kutero koma anthu angawakhulupilile bwanji achilima pomwe nawonso adakali m’boma lomwe akuti ndilakubalo, apa ,ikusonyeza kuti achilima ndiosakhwima pa ndale kotero zitha kuwavuta kwambiri pochoka mu DDP chifukwa anthu anzelu azindikila kuti iwowa ndikadzitape pa ndale.

Comments are closed.