Muli Afarisi muno – Mutharika

Peter Mutharika

A Chilima ndi anthu ena onse amene akunena kuti a Mutharika apume ndi anthu a bizinesi ndipo akufuna kugulitsa chipani, atelo a Mutharika.

Pa mwambo otsegulila trade fair mu mzinda wa Blantyre, a Mutharika anasintha nkhani ndi kuyamba kulubwalubwa za ndale.

Peter Mutharika
Mutharika pa mwambo otsegulila trade fair.

Mu mawu awo a Mutharika ananena kuti pali anthu ena mu chipani cha DPP amene akufuna kuononga chipani cha DPP pomema a Mutharika kuti achoke.

A Mutharika anafanizila anthu otele ku Afarisi amene ntchito yawo inali yotonza Yesu.

Gulu lina mu chipani cha DPP lakhala likunena kuti likufuna a Mutharika atule pansi udindo ndi cholinga choti achiwiri awo a Saulos Chilima a zaka 45 atenge udindo.

A Mutharika akhala akunena motsindika kuti iwo ndiwo ali ndi kuthekela kotenga DPP mu chisankho cha 2019 ndinso kupambana chisankhochi.

Advertisement

2 Comments

  1. Kodi nkhani zoti President Munthalika atule pasi udindo zinayamba kumveka mwezi watha komano vuto a chilima sakuyakhulapo chilichose zakhaniyi akutatha uza chani chifukwa zikanakhala kuti sakungwilizana nawo anthu amenewa bwezi atabwera poyela ndikuwauza anthu kuti sakufuna kutelo komano chete wake ameneyu zikuonesa kuti udindo umenewu akufuna kwambiri chifukwa ma President onse alamulira dziko la mw sanapangidwepo zimenezi kapena mukufuna kupeleka Chipani kwa anthu osusa please stand up and say something to the people of malawi

Comments are closed.