Kwatsala tchire:maule ndiye zawo zayenda

Advertisement
Jabulani Linje

Ndi lerotu neba pa Balaka. Kukakhala ku banja la maule, usikuwu anagona tulo tofa nato podziwa kuti malo awo mu ma semi alipo kale. Palibe olanda.

Nyerere kapena kuti manoma ali ndi ntchito yaikulu lero pamene akukumana ndi Kamuzu Barracks ku Balaka mu chikho cha Airtel Top 8.

Mu masewelo oyamba amene anachitikila mu mzinda wa Lilongwe, manoma anamwetsa chimodzi chokha kuti akhaleko ngati achenjelera KB.

Lero KB nayo ikuoneka kuti sinavomele zogonja ndipo ichita mavuvu kuti mwina ndi kutembenuza zinthu.

Masewelowa akuyembekezeleka kukhala okoma maka poti akubwela pa nthawi imene maneba a Noma, maule adutsa kale atatulutsa Moyale.

Maule adaswa Moyale ndi chigoli chimodzi kwa duu pa masewelo awo oyamba pa Kalulu. Pa masewelo achiwiri mu mzinda wa Mzuzu, maule ndi Moyale analepherana osamwetsana olo chigoli chimodzi.

Kodi nazo nyerere zingachite umu achitila Maule? Zioneka lero.

Advertisement