Ku nkhondo ya ku DPP, ana a mma Yunivesite ali mbali ya Mutharika

4

Nkhondo ija ya Absalom ndi Davite yavuta ku chipani cholamula cha DPP. Ndipo pamene aliyense akukokela mbali yake, nawo ana a mu sukulu za ukachenjede ati asatsalire.

Ana a mu sukulu za ukachenjede a chipani cha DPP auza Mtsogoleri wa dziko lino a Peter Mutharika kuti iwo akufuna a Mutharika ayimile chipani cha DPP mu 2019.

Peter mutharika

Ana a mu sukulu za ukachenjede a chipani cha DPP asankha a Mutharika.

Iwo anena izi pamene anakumana ndi a Mutharika ku Sanjika pa nthawi imene mu chipani cha DPP anthu ena akhala akufuna kuti a Mutharika atule pansi udindo kuti m’malo mwawo pabwele a Chilima amene akuti ndi wa chinyamata.

Koma polankhulapo pa nkhaniyi, atsogoleri a ana asukuluwa ananena kuti anthu onse ofuna kuti a Mutharika azisiye ndi anthu okhumudwa chabe.

Iwo anaonjezelapo kuti anthu onse a chipani cha DPP mtima wawo uli pa a Mutharika.

Polankhulapo a Mutharika anatsimikizila ana asukuluwo kuti iwo ayima 2019 pa tiketi ya DPP ndipo onse ofuna kuti iwo achoke alemba mmadzi.

 

Share.

4 Comments

  1. Iiiiiiiiii, koma abale pali ndalama-Eeeeeee, simanamadi . Tima k20 000 tomwe mwalandilati mpakana basi mwakopeka kugulitsa ufulu wanu wosankha yemwe mukufuna ?

  2. Munthu ukakura ndibwino kupuma kuti ulandire ulemu, mesa amati achinyamata ndi atsogoleri amawa? nanga mawa lizakwana liti ngati okalamba sakupeleka mpata? okusapotaniwo choonadi akuchidziwa koma akungofuna akudyeleniko kaye timakhobidi.

%d bloggers like this: