Mikangano yatha ku MCP

Lazarus Chakwera

Inu a DPP, zichedwani ndi kulumana. Anzanu a Kongeresi ndiye zawo zayela anga achapa ndi Boom.

Zija zomati a Kaliwo, a Msowoya ndi a Kabwila akatenga chiletso kapena apilikitsidwa mu chipani, ndi nkhani yakale tsopano. Simuzivanso.

Lazarus Chakwera
Chipani cha MCP chasankha a Chakwera kuti ndiwo akhale Mtsogoleri wa chipanichi.

Chipani chotsutsa cha Kongeresi chasankha anthu amene akhale akuchitsogolera pa ulendo wa 2019 ofuna kutsomphola boma kuchoka kwa a DPP.

Pa mwambo umene unachitika dzulo mu mzinda wa Lilongwe, chipani cha MCP chasankha a Lazarus Chakwera kuti ndiwo akhale Mtsogoleri wa chipanichi ndipo azachiyimila mu 2019.

A Chakwera akhala ndi achiwiri awiri, oyamba ndi a Sidik Mia ndipo wachiwiri kwa wachiwiri ndi a Harry Mkandawire.

Mwambowu unabwela patatha nthawi kamba kakukokanakokana komwe kumachitika mchipanichi.

Advertisement

4 Comments

  1. Ndiye ziugwirizana ndi zomwe mwalemba kumayambiriroko?? Anthu mwawatchula kuti anapitikitsidwawo analiko?

Comments are closed.