Bushiri hailed in RSA.

National

Bushiri amangidwa

By Kondwani Mkhalipi-Manyungwa

May 07, 2018

M’busa amene amaziti ndi mneneri Shepherd Bushiri analowa mchitolokosi cha a Polisi m’dziko la South Africa usiku wa loweruka.

Bushiri amene akufufuzidwa pa mlandu okuba ndalama ku South Africa kuti azizabisa ku Malawi kuno, anaitanidwa ndi a Polisi a ku joweni pa nkhani ina.

Bushiri analowa mchitolokosi cha a Polisi usiku wa loweruka.

A Bushiri ati asumilidwa ndi mzimayi wina mdzikomo pa mlandu oti anamuonongela mbiri.

Mayiyo adadandaula kuti a Bushiri mu tchalitchi chawo anamutchula kuti iye ndi mfiti ndipo zinamuonongela mbiri ndi malonda.

A Polisi anapita ku mpingo wa a Bushiri mkati mwa sabata yatha koma ati abusa a mpingo wawo ndi anthu oteteza a Bushiri anawagwilagwila.

Loweluka usiku a Bushiri anakazipeleka ku Polisi komwe anadziwitsidwa za mlandu wawo.