Zako izo, ife timwa mowa ndi kukwatila mmene tingathele: Angoni a ku Mzimba sakuifila CCAP

Inkosi ya Makosi Mbelwa

Inkosi ya Makosi Mmbelwa, imene ndi Mfumu yaikulu ya Angoni, yadzudzula a Livingstonia Synod ndi kuwachenjeza kuti akapanda kusamala athamangitsidwa mu dera lake.

Pa mwambo oveka ufumu a T/A Mzukuzuku ku Mzimba, mlembi wamkulu wa Synod ya Livingstonia a Levi Nyondo anadzudzula Mafumu a chingoni ati kamba komwa mowa ndi kukwatila mitala.

Inkosi ya Makosi Mmbelwa

A Nyondo anaonjezelaponso kuti Mafumu ena amalimbikitsa anthu awo kuchita ziwirizo ngakhale amadziwa kuti ndi tchimo ndipo ndi zosaloledwa mu mpingo wa CCAP.

Pamene a Nyondo amanena izi ndikuti anthu mmbalimu akuwakuwiza.

Ataima ndi kuyankhulapo Inkosi Mmbelwa anadzudzula a Synod kuti asamayankhule mwa thamo pamaso pa Mafumu.

“Ife ngati Mafumu sitilakwa, ikakhala nkhani ya mowa ndi akazi ikukambidwa apayi, ndi chikhalidwe chathu,” anatelo Mmbelwa.

Mmbelwa anakumbutsa a mpingo kuti iwo anapeza anthu a chingoni akumwa mowa ndi kuchita mitala.

“Sitinali ife kupita kwa mpingo kukapempha mgwilizano ayi. A mpingo anatipeza ndi kuvomeleza kuti tizipanga chikhalidwe chathu tili ma membala awo, lero asasinthe,” anatelo Mmbelwa.

Kenako anachenjeza kuti akapanda kusamala, a mpingo atha kuthamangitsidwa mu dera lake.

 

Advertisement