Mutharika aimila DPP mu 2019

Peter Mutharika

Ati za Chilima muiwale. Ngati aimile ndiye mwina chipani china basi koma kuja ku DPP, palibe amene akufuna a Mutharika achoke. Anthu ali nganganga pambuyo pa a Mutharika.

Komiti yaikulu ya chipani cholamula cha DPP yatsindika kuti iwo agwilizana kuti a Peter Mutharika apitilize utsogoleri wa chipani chawo maka pa chisankho cha 2019.

Peter Mutharika
Komiti yaikulu ya chipani cha DPP yati a Mutharika aimila DPP mu 2019.

Pa msonkhano wa atolankhani umene anachititsa dzulo mu mzinda wa Lilongwe, akuluakulu a chipanichi anati ngakhale iwo sanachititse convention koma anali odziwa kuti anthu ambiri ku chipani anali ofuna kuti a Mutharika apitilize.

Poyankhulapo pa maganizo a ma membala ena a chipanichi amene anena kuti a Mutharika asapitilize ndipo m’malo mwawo pabwele a Chilima, akuluakulu a chipanichi ananena kuti awo ndi maganizo a anthu ochepa mu chipanichi ndipo nawo ali ndi ufulu otelo ndithu.

Pa nkhani ya amene azayime ndi a Mutharika mu 2019, akuluakulu a chipanichi anakana kunena ati kamba osankha munthu ameneyo ndiye oimila chipanichi amene padakali pano ndi a Mutharika.

Advertisement