Bola Chilima: Callista Mutharika ati alamu ake Peter asayimenso 2019

Waika mutu wake pa njanji mkazi wa Mtsogoleri wakale wa dziko lino a Callista Mutharika. Wangochita za Yobu 13:13, kutayila uko ubale wake ndi Mtsogoleri wa dziko lino a Peter Mutharika. Iwo ati kwa iwo bola Malawi basi.

Mayi Callista Mutharika amene ndi alamu awo a Mtsogoleri wa dziko lino a Peter Mutharika ati iwo akufuna wachiwiri kwa Mtsogoleri wa dziko lino a Saulos Chilima azaimile DPP mu 2019.

Mutharika akuti bola ataima a Chilima

Mu kulemba kwawo pa gulu la aphungu akale la pa utatavu wa Watsapu, a Callista ati iwo 2019 sakufuna kuonanso nkhope ya a Peter Mutharika pa oyimila chipani cha DPP.

“Kuti dziko lino lipite patsogolo, ku DPP kuja atenge Chilima basi,” anatelo a Mutharika.

Zonena zawo zadza pamene kunamveka mphekesela kapena kuti ulosi oti a Mutharika azitaya ndale mu 2019 ndipo asankha munthu wina m’malo mwawo.

Komatu a Mutharika akhala akunena mobwelezabweleza kuti 2019 iwo akuima ndipo apambana modetsa nkhawa.

Advertisement

9 Comments

  1. But Peter publicly promised that he will never let you walk alone. Zatani Kalisita lero kuti umuchitise manyazi Afana pa malawi media? Umayesa akubakila kuti utenge Ndata. Mkazi osakhutusidwa komanso omvetsa chisoni.

  2. Amkawona ngati alowedwa chokolo mzimayiyu nsanje ndi nzake Getrude.

  3. Kodi a Callista ndi a DPP? Ngati ali mu Dpp ali ndi udindo wanji?

Comments are closed.