Iwalani kaye za Konveshoni – Chakwera

Advertisement
Lazarus Chakwera.

A Kongeresi kodi mulipo apa? Musapite kutali chifukwa tili ndi uthenga wanu. Zija za Konveshoni mumadikila zija kuti ichitika lero pa 5, ku Mzuzu, ati muziiwale kaye.

Mtsogoleri wa chipani chotsutsa cha MCP, a Lazarus Chakwera wauza anthu otsatila chipanichi kuti msonkhano waukulu wa chipanichi wayamba waimitsidwa kaye.

Lazarus Chakwera.
Chakwera: Tikazathana ndi nkhani izi zili ku Khoti ndipamene tizakambe za Konveshoni.

Mu chikalata chimene a Malawi24 taona, a Chakwera ati chimkulilano chimene chavuta mu chipanichi ndicho chapangitsa kuti ayimike kaye Konveshoni yawo.

“Kuli milandu mpwechempweche ku mabwalo athu a milandu, ena atitengela ziletso. Ife sitinyozela zigamulo za Khoti ayi, tikazathana ndi nkhani izi zili ku Khoti ndipamene tizakambe za Konveshoni,” watelo Chakwera mu chikalata.

Mpungwepungwe mu chipani cha Kongeresi udayamba pamene a Chakwera adasintha thabwa ndi kusonyeza kuti iwo akufuna kuzapikisana pa chisankho cha 2019 ndi a Sidik Mia, osati a Richard Msowoya amene anapikisana nawo pa chisankho cha 2014.

Mkangano utakula mu chipanimu, a Chakwera adaganiza zothothola mu chipani a Msowoya ndi anthu amene akuwamvela chisoni monga a Gustav Kaliwo, a Jessie Kabwila ndi a Tony Kandiero.

Anthuwa adakamang’ala ku Khoti kumene anawapatsa chiletso.

Advertisement

2 Comments

  1. lets unit we are all one zokangana zimabwezeletsa chitukuko mdziko, mmalo mokopa anthu mukukangana nokhanokha why?

  2. It is stupidity of any party leader to discard long-time members in favour of newcomers. Miayo ngati amadzithemba, osayambitsa chipani chake bwanji? Anzake MCP ayinvutikila, iye akufuna kungotola? Zizitheka.

Comments are closed.