Akazi aku Malawi samatha kuyamikira amuna – atero Tay Grin

Namanyonyolo pa nkhani ya mayimbidwe Tay Grin wanena mosaphyatira kuti atsikana a ku Malawi samatha kuyamikira mphongo ngakhale itakhala yooneka bwino motani.

Tay Grin amene dzina lake lenileni ndi Limbani Kalilani wanena izi masiku awiri apitawo kudzera pa makina a intanenti amene anthu amaika ndikuonapo zinthunzi a insitagalamu.

Tay Grin wati akazi aku Malawi sangauze mamuna kuti ndiooneka bwino.

Muuthenga wake omwe anaulemba mwanthabwala anati chomwe akazi akumudzi kuno amatha ndikukuweruza moipa malingana ndi maonekedwe ako.

“Malawian girls will never tell you that you are handsome (akazi aku Malawi sangauze mamuna kuti ndiooneka bwino) basi amvekere, nkhope yakoyi wayenera kukhala okonda akazi iwe,” anatero Tay Grin.

Ngakhale izi zinali nthabwala chabe, anthu ena mu dziko lino sanakondwere nazo ponena kuti zikupereka chithunzi choipa cha akazi a ku Malawi. Ndipo ati Kalilani akuyenera kumanena za bwino za anthu a dziko lake, monga munthu amene amanyamula mbendera ya dziko lino.

Pamene ena sanazitengere nthabwala za oyimbayu ponena kuti nayeso ndi munthu ndipo nthawi zina amayenera asekesepo anthu.

Advertisement

3 Comments

Comments are closed.