Kulibe Jehena – watelo Papa

Advertisement
Pope Francis: There is no hell

Heeee okumwa tiyeni timwe mwa mtudzu! Otamba, ufitiwo onetsetsani mukuwupanga ngati mulandila malipilo mwezi ukatha. Inu achigololo, musaleke ponyani giya. Pamapeto pa zonse, ati ngati simulapa muzangosowa basi. Si za ku Jahena iyayi.

Pope Francis: There is no hell
Papa: Kulibe Jehena

Malinga ndi malipoti amene mpingo wa Katolika ukutsutsa, Mtsogoleri wa mpingowu pa dziko lonse a Papa ati anena kuti Jahena kulibe.

Malinga ndi nyuzipepala ya mu dziko la Italy ya _La Republicca_ ati mkulu wa mpingo wa Katolika anauza mwini wa nyuziyi kuti nkhani za Jahena ndi ntchetera.

“Inu, Jahena kulibe,” ati a Papa anatelo. “Anthu ochimwa akuyenela kulapa, akalapa ndiye akalowa kumwamba. Koma ngati salapa, mizimu yawo izasowa basi. Osapezekanso.”

Mtolankhani anauzidwa izi ati ndi mzawo wa pamtima wa a Papa wa zaka 93 ndipo ndi osakhulupilila zoti kuli Mulungu.

Ndipo akuluakulu a mpingo wa Katolika atsutsa nkhani iyi kunena kuti nyuzipepala yalemba bodza.

“A Papa sanakambepo zimenezo, ndi bodza la nkunkhuniza. Mtolankhani uyu sanawamvetse,” atelo akuluakulu a ku Vatican.

Advertisement