Kutchuka kunandisandutsa mbiyang’ambe – atero Martse

Advertisement
Martse

Katswiri oyimba nyimbo za chitawuni Martin Nkhata amene amadziwika ndi dzina lodyera loti Martse wabwera poyera nkunena kuti kutchuka kunamusandutsa mbiyang’ambe.

Martse waulura izi dzulo kudzera pa tsamba lake la Facebook ndipo iyeyo walangiza anthu kuti asadzakhale ngati iyeyo potengera kuti kutchuka kumamupangisa zinthu zoipa.

Martse
Martse kutchuka kukundisautsa koopsya.

Katswiriyu amene amakhala mu mzinda wa Lilongwe wadandaulanso kuti chifukwa cha kutchuka, anasiya kucheza ndi anzake ena, anayamba kusuta fodya wamkulu, kupanga zidani ndi anthu komaso adatsala pang’ono kusiya sukulu.

Ndipo Nkhata watsindika mozimvera chisoni kuti ngakhale ali odziwika ndi dziko, moyo wake ngati munthu wa za msangulutso sumusangalatsa.

Ndipo mukulongosola kwake akuti awa ndi malipiro a kutchuka amene akumusautsa koopsya.
Choncho wapereka langizo kwa mtundu wa a Malawi kuti azipempha nzeru kwa chisumphi kuti aziatsogolera mu zokhumba zawo.

Martin amene anatchuka ndi nyimbo yoti Mwano pano akunenedwa kuti akutha ngati makatani potengera kuti nyimbo zake sizikutchukaso ngati kale.

Advertisement

One Comment

Comments are closed.