Anamanyonyolo pa maimbidwe akwezedwa mu mtengo wa malambe

Slessor Munthali

Zatsimikizika kuti akatswiri ena pankhani ya mayimbidwe mu dziko lino akwezedwa mu mtengo wa malambe.

Zaululika kuti oyimbawa; Slessor Munthali, Blaze, Stich Fray, Blackjack, Marcus ndi GD, ndiamene akwezedwa mu mtengo wu. Ndipo zamvekaso kuti iwowa achita kuthandizidwa ndi oyimba nzawo otchedwa Young D.

Young D
Young D

A katswiriwa, athandiza Young D kuimbaso nyimbo yake yomwe yatchuka kwambiri yotchedwa Mtengo wa Malambe. Ndipo mwini wake nyimbo yu watsimikizira Malawi24 za Nkhaniyi.

Young D adauza Malaw24 tsiku lolemba kuti iyeyo anasankha kuimbira limodzi ndi akatswiri wa chifukwa Namalenga anadzadza zikho zawo ndi luso, mpaka kufika posefukira.

“Nditaona ukatakwe wa akamuna amenewa mu mayimbidwe ndinaganiza kuti ndigwire nawo ntchito limodzi,” anatero oyimba yu.

Iye ananenanso kuti potengera kusiya kwa zamba zomwe amaimba a katalangwewa, adachiona chanzeru kuti abwerese pamodzi ma luso osiyanasiyana. Ndipo iyeyu wanenesa kuti izi sizisintha kuzuna kwa nyimbo ya Mtengo wa Malambe.

Nyimbo imeneyi yomwe ikukondedwa kwambiri ndi a Malawi inatuluka koyamba mu chaka cha 2016. Ndipo kanema wake amene anajambulidwa mwa luso wakhala akupambana pa mindandanda ya nyimbo yosiyanasiyana mdziko muno.

Mtengo wa Malambe omwe watenderedwa ndi a katakwewo ukuyembekezereka kutuluka kumapeto kwa mwezi uno.

 

Advertisement

3 Comments

Comments are closed.