Abusa a Ziba amangidwa kamba koba msonkho

Joseph Ziba

Bukhu loyera Mateyu 22 vesi la 21 Akhristu ambiri akulidziwa ndipo akuyenela kuchita umo linenela.

M’busa otchuka mu mzinda wa Blantyre, a Joseph Ziba amangidwa ati kamba kothawa kupeleka msonkho okwana 26 miliyoni Kwacha.

Joseph Ziba
Akwizingidwa

Malinga ndi malipoti, a Ziba anagula galimoto lapamwamba kwa mmwenye wina Tayub Aziz imene inali yosalipilidwa msonkho.

Bungwe la misonkho litapeza a Ziba kuti alipile msonkho wa 26 miliyoni pa galimotoyo, ati iwo koyamba anavomela.

Koma kenako anachita ukambelembele ndi kupita ku khoti kukatenga chiletso kuti a bungwe la msonkho asawalande galimoto kapena kuwakakamiza kulipila.

Atazindikila za njomba yomwe munthu wa Chautayu anachita, a bungwe la misonkho nawo anapita kukhoti komweko kukapempha kuti achotse chiletso chija. Izi zinatheka.

Ndipo akuti dzulo Apolisi pamodzi ndi a bungwe la misonkho ananjata abusa a Ziba pamodzi ndi mzawo anawagulitsa galimotoyo.

Advertisement

22 Comments

  1. This is what we call Bad or Wrong reporting. If this is what we would expect from journalist, then it is only right to change jobs.

  2. Abusa ngati zili choncho ayi munalakwitsa chifukwa satana salimbana ndi anthu ake amalimbana ndi ana a Yehova chonchonso munthu wamulungu akalakwitsa nkhani imathamanga kwambiri than yamunthu osakhulupirira komabe sibwino kuti tikuweluzeni chifukwa nthawi zina anthu antha kunena zambiri koma chilungamo chake mukuchidziwa ndiinu ndi Yehova wanu chilungamo chioneka.Yehova akuthandizeni munyengo yowawitsayi

  3. zachamba basi tamaleni zoveka bwino kale mumati wamangidwa chifukwa galimoto yake sanasonkhele msonkho

  4. ubwino wake wanena akhristu osati asilamu kut akulidziwa ndiye ife zisatikhuze zanuzo athana nazo okha

    1. Nawe tazingodikilira tsiku lolandila mitu ya mbuzi mmipanda mwa amwenyemu, ngati sizikukhuza ukulowelera bwanji? Pita ukapempherere amwenyemu akupatse 200 kugulitsa pemphero

    2. musova man simunati or chopeleka mupeleka ndi abakha omwe koma sizikwanira pa figure yomwe akufuna a custom m ‘ busa wanji othawa misokho

Comments are closed.