Nkhanza za Chakwera zandipititsa ku DPP – Jumbe


Felix-Jumbe

Wazitaya. Wazinyanyala. Wazidomoka. Wayendela yake. Wapita atanyangala ndipo walalika kuti a Chakwera ndi munthu wa nkhanza asananyamuke.

Phungu wa dera lapakati mu boma la Salima a Felix Jumbe alengeza kuti tsopano alowa chipani cholamula cha DPP.

Felix-Jumbe
a Jumbe alowa chipani cha DPP

A Jumbe alengeza izi kudzela pa tsamba lawo la Facebook kuti tsopano iwo ndi a chipani cholamula ndipo mu 2019, iwo akuima ngati wa DPP.

A Jumbe anenanso kuti iwo sazaimanso ku dera lawo lapano, ati m’malo mwake akukayima ku dera la kumpoto mu boma la Salima lomwelo komwe kuli kwa Mayi awo.

Atauzidwa kuti iwo akagonja kumene akupitako kamba koti DPP ilibe chikoka, a Jumbe adanena kuti anthu ndiwo awatuma.

A Jumbe adachotsedwa mu chipani cha Kongeresi mu chaka cha 2016.

Ngakhale adatenga chiletso ku bwalo la milandu, a Jumbe ndi Kongeresi akhalila kulumana.

 

172 thoughts on “Nkhanza za Chakwera zandipititsa ku DPP – Jumbe

  1. Its a bit late,go and finish yourself that side,here we don’t worship idols I can clearly c ur downfall

  2. kumangoomberam’manja ndizitsiruzomwe ngatiJumbeyo aDPP mukusowaanthu? tifuseni ife akuSalima Central, tikuuzenizagaluyo

  3. Pepani pitani bwino osaononga dzina lanu.We need true leaders.Chipani sichamunthu amodzi.Achinyamata alowapo mwachokapo.Ndale zabwino Malawi wabwino.But Ku DPP akusalani achimwene!!!

  4. Mbava zakumalawi ntchito kuba ndalama yamalawi,inu ajumbe muzakhutisidwa lit popeza anthu nonse okuba muli pafupi ndi zenje lamantha.muona mulungu akukhandani.

  5. Love it, hate it. It’s still a gain to DPP. Can MCP tackle the 50+1 electoral reforms? Definitely no. Slowly its bargaining power is reducing on the electorate.

  6. Zabwino zonse bwana…….koma muzisiya phazi osasiya mulomo. Dzikoli kapena moyowu uli ngati pelete Wa asilikali. Imafika nthawi ya about turn!!!!!!!!

Comments are closed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading