Ati kwawo kwatha. Ngati kuli kusolola, asolola basi ndipo amaliza. Tsopano ndi nthawi ya Kongeresi.
A Sidik Mia amene analowa chipani cha Kongeresi auza anthu a DPP kuti alongeze katundu wawo mmboma chifukwa 2019 kulibe kubwelelamo.
A Mia amene akuyembekezeka kuzakhala wachiwiri wa a Chakwera pa chisankho cha 2019 ati Kongeresi itenga boma basi.

A Mia ati a Chakwera ndiwo akhale Mtsogoleri wa dziko lino kuyambila 2019 ndipo achita zitukuko zodula mutu.
Iwo anadzudzula boma la DPP ati kamba kolephera kutukula dziko lino mu zaka zinayi zomwe akhala pa udindo ndipo m’malo mwake ayamba kujijilika pano kuyala miyala ya maziko.
“Pa zaka zinayi alephera kupeleka mwayi wa ntchito ku achinyamata, alephera kutukula dziko lino ndiye lero akati tiwavotelenso? Akunama,” anatelo a Mia.
A Mia ananena kuti boma la Mutharika tsopano likuyenela kulongeza katundu wawo ndikuyamba ulendo osamuka mmboma.
160 thoughts on “Longezani muzipita ku Ndata – Mia auza a DPP”
Comments are closed.

Mia usavutike ukaonjeza mwano even ndi MP omwe suzawina,DPP boma
MCP boma
Mia political prostitute,ungatiuze chani iwe… Nonse ndi mbava
kongeresi lero! Nthawi ya MCP inatha kalekale and chipanichi chinapita ndi kamuzu
aaah amia asaxipusiE makaladi tuwaziwa ife palibe game amasewela osaikapo juga azavoteledwa ndi asena nda chewa ananjoya nthawi ya gogo wankhaza uja
DZUKA MALAWI DZUKA……….ANTHU MUMENE MUKUVUTIKIRA KUMALAWIKO BASI MUDAKALI KUSAPOTA DPP????? OOOOO SHAME ON YOU PLZZZ………WINA WACHITA KULEMBA KUTI DPP YIZALAMULIRA MUPAKA 1000 YEARS …….MWINA YIZALAMULIRA AGOGO AKO STUPID!!!!
Mr Mia Tsekani Kamwa Yanu Musathe Mau Mwayenda Zipani Zingati Inu?
Pandale aliyese amayakhula zimene aķuona kut angathe kutero chocho amia anena mbali yao kuti awina ndio ndiye nao a dpp akut nafe tiwinaso ndie inu o komenta zikumaoneka kut aliyese akukokera mbali yake apa koma sinu andale mumangovota osewa anal chipani chimozi achita kumasitha ndie tieni tidikire 90mins
IWE MIA MANYI AKOWO UZIWAUZA AZAMBUYAKO
Amalawi 24 werengani ma Vote APA tiwone amene waluza! Zikuwoneka kuti A mia agwa nayo!
Kumbwambwana
MCP all the way….2019 osalakwitsa…
DPP titchecha ndi mitsitsi yomwe ovotafe tiliphee tingonola zikwanje zathu.
Mia chilimikani kwambili tili mmbuyomo 2019 MCP boma basi enawa apite akalime ku ndata.Abe anthu ma alubino akhale ndimntendele paumoyo wawo
Dpp or zinthu zitavuta maka singawine, oziwa ndale amawelengela,NOTE DPP IZAWINA KU THYOLO NDI MULANJE PANG’ONO BASI.you will mark my words.
This z wat we call old school politics…dissing each other cant helf .Mr Mia just tell wat u will to wen u takeover the goverment…
Amia asathe mau
Mia ndiodwala.bola azinena azizakeo. ndipo Mia ndiwa business osati ndale .
Ndipo zoona zake zimezo
Hahaha azikamba ena osati bambo MIA