Longezani muzipita ku Ndata – Mia auza a DPP

160

Ati kwawo kwatha. Ngati kuli kusolola, asolola basi ndipo amaliza. Tsopano ndi nthawi ya Kongeresi.

A Sidik Mia amene analowa chipani cha Kongeresi auza anthu a DPP kuti alongeze katundu wawo mmboma chifukwa 2019 kulibe kubwelelamo.

A Mia amene akuyembekezeka kuzakhala wachiwiri wa a Chakwera pa chisankho cha 2019 ati Kongeresi itenga boma basi.

Sidik Mia

Mia: Boma la a Mutharika lalephera.

A Mia ati a Chakwera ndiwo akhale Mtsogoleri wa dziko lino kuyambila 2019 ndipo achita zitukuko zodula mutu.

Iwo anadzudzula boma la DPP ati kamba kolephera kutukula dziko lino mu zaka zinayi zomwe akhala pa udindo ndipo m’malo mwake ayamba kujijilika pano kuyala miyala ya maziko.

“Pa zaka zinayi alephera kupeleka mwayi wa ntchito ku achinyamata, alephera kutukula dziko lino ndiye lero akati tiwavotelenso? Akunama,” anatelo a Mia.

A Mia ananena kuti boma la Mutharika tsopano likuyenela kulongeza katundu wawo ndikuyamba ulendo osamuka mmboma.

Share.
  • Opinion