Munthu ndi m’chemwali wake amangidwa kamba kochita chiwerewere pachibale

2

…mpaka anabeleka ana awiri

Zina ukamva, thupi lonse limagwidwa nyetsi.

Munthu ndi mlongo wake amangidwa kwa chaka ndi theka zitadziwika kuti amazembelana mpaka kufika popatsana mimba kawiri ndi kubeleka ana.

Malinga ndi nyuzipepala ina ya mu dziko la Zimbabwe, ati Khoti mu dzikoli lalamula awiriwa kuti akasewenze kundende kwa chaka chimodzi ndi theka.

MangochiAwiriwo ati ali ndi Mayi ofanana koma Bambo osiyana ngakhale amakhala nyumba imodzi.

Nkhaniyi itadziwika kuti awiriwa amatchetchelelana ngakhale chili chibale ndithu, Apolisi analowelelapo ndi kuwanjata.

Iwo anavomela kuti amagonana ndithu ndipo ana onse awiri amene msungwanayo ali nawo ndi ake a mnyamatayo.

Apa a bwalo sanachitile mwina koma kuwagamula awiriwa kuti akatsekeledwe kwa zaka ziwiri. Koma miyezi isanu ndi umodzi anachotselapo ati kamba uwu unali mlandu wawo oyamba.

Awiriwa ndi a Never Chitisiga a zaka 27 ndi mlongo wawo a Christine Mudyanengava a zaka 21. Iwowa amachokela ku Chitungwiza.

 

Share.

2 Comments