Kulibe za CAF kwa nyerere, pezani zina zochita basi

Advertisement
Super League Malawi

Aiopela kutali. Olo asanaugunde mpira ndi komwe azitaya. Za CAF zija sanali maloto koma zilubwe. Pano mukamuona mzanu wa nyerere, musayambitse ya CAF mudana, ingokambani ya Super League.

Super League Malawi
Pezani zina zochita basi

Masiku atangotsala pang’ono kuti nyerere zikaponde ku DRC mu chikho cha CAF, izo zalembela FAM kuti sizipita. Ati zawakulila.

Malipoti ati mlembi wamkulu wa nyerere a Mike Butao alembela bungwe la FAM kuti lidziwitse a CAF kuti nyerere zalephera basi kupita ku CAF.

Mavuto a zachuma ndiwo anthu akuti athetsa maloto a nyerere. Masiku apitawa timuyi inayamba kupemphetsa koma zikuoneka ngati sizinaphule kanthu.

Lero mmawa kunamveka kuti othandiza timuyi a Be Forward analangiza akulu akulu a timuyi kuti za CAF azisiye, asalimbane ndi mtunda opanda madzi.

Pamwamba pake zinamveka kuti ku nyerere kumene kunali chipwilikiti pamene osewela ananena kuti iwo sapitiliza zokonzekela za CAF.

Pofika masana zinatsimikizika kuti nyerere zazitaya za CAF.

A CAF akuyenela kupeleka chilango kwa nyerere.

Advertisement

43 Comments

  1. Ana Achepa Caf Sizocheza Imafunika Sposa Yachuma Ost Yaumakaniko Yokoza Magalimoto Akufa Kkkkkkkkkkk Nbb Woyeeeeeeee Zamanyazi Ku Kapado Kapena Kut Kakozo Fc

  2. Zinawoneka!,nanga mapreparations angapange ndi mangochi select!,komanso kupanga draw chonsecho penalty!,ayi apo ndiye mwawonetsa kulimba mtima kubwera poyera kuti sitikwanitsa!,ali ena akanapita nkukarandirako 10 kwa zilo!,ayi takunyadirani!”ZONSE ZIMAYAMBA NDI MANOMA “,apanso mwatiyambira kulephera mutalembetsa!

Comments are closed.