A Malawi oposa zana athamangitsidwa ku Sasafulika: ambiri ndi a ku Mangochi ndi ku Mzimba

Advertisement

Abwelako ku Joni opanda kanthu. Angobwela ndi zovala zapathupi pawo ndi kaselula basi. Kaya ayambila pati kumudzi kuno?

A Malawi okwana zana limodzi ndi theka kudza mphambu imodzi (151) afika m’dziko muno atathamangitsidwa ku South Africa komwe amakhala opanda chilolezo.

A Malawi awa afika Lolemba pa 29 kudzela pa bwalo la ndege la Kamuzu International mu mzinda wa Lilongwe.

Malinga ndi mneneri wa bwalo la ndege la Kamuzu International, a Martin Gondolo, abambo okwana 149 ndi amayi awiri ndiwo anafika m’dziko muno atatopa ndi kukhala pa malo a Lindera podikila kubwela kumudzi.

Umboni umene tapeza a Malawi24 waonetsa kuti pa a Malawi omwe afika m’dziko muno, ochuluka akuchokela mu boma la Mangochi ndipo kenako Mzimba.

Pa a Malawi 151, 62 ndi ochokela mu boma la Mangochi, 41 ndi a ku Mzimba, 5 ndi a mu Blantyre, 11 a ku Machinga, 7 kuchoka ku Nkhatabay, 4 ku Dedza, 7 ku Mulanje, 5 ku Chiradzulu, 8 ku Zomba and mmodzi wa ku Nsanje.

Chaka chatha mu mwezi wa December a Malawi ena 72 anafika mu dziko muno atathamangitsidwa mu dziko la Zimbabwe kamba kokhala opanda chilolezo.