Musaope, gumulani nyumba zonse zomangidwa mu phiri – Khoti liuza a khonsolo ya Blantyre


Soche

Bwalo lalikulu la Milandu tsopano lamasula khonsolo ya mzinda wa Blantyre kuti ndi yololedwa kugwetsa nyumba zonse zomwe zamangidwa mu phiri.

Khonsolo ya mu mzinda wa Blantyre inauza anthu onse omanga nyumba mu phiri kuti asamuke. Koma anthu aja m’malo mosamuka anapita ku Khoti kukatenga chiletso.

Anthony Kasunda
Kasunda

Kwa zaka zisanu, a khonsolo akhala asakuchita kanthu ati kamba ka chiletsocho. Koma tsopano chiletso chija chachotsedwa.

Ndipo tsopano a khonsolo apeleka chenjezo kwa anthu amene akukhala mu mapiri a Soche, Ndirande kudzanso Mpingwe kuti asamuke ndi kugwetsa nyumba zawo.

“Ali ndi masiku 60 anthu amenewa, miyezi iwiri yeniyeni. Ikatha tikubwela tokha ndi galimoto zathu kuzasalaza,” anatelo mneneri wa Khonsolo a Anthony Kasunda.

A Kasunda ananenanso kuti a khonsolo apeleka malo kwa anthu 65 amene asamuke.

Iwo anati pamene nkhaniyi imayamba, anali ma banja 65 okha amene amakhala ku phiri.

“Tsopano alipo 300, koma enawo anabwela akudziwa kuti malowa ndi osaloledwa kukhala,” iwo anatelo.

 

 

69 thoughts on “Musaope, gumulani nyumba zonse zomangidwa mu phiri – Khoti liuza a khonsolo ya Blantyre

  1. Kubwezelesa chitukuko mmbuyo bwanji munthu wamanga nyumba yake inu nde mugumuleso? Tamayendani a Malawi muziona mmayiko anzathu nyumba dzao kuti zili kuti pamwamba penipeni pa phili boma ndikwasatilaso komweko ndinseu opambana kwambili koma kumalawi iiiiiii mmmmh

  2. Malo ake omwewa a Chauta Namalengawa mukuti ndi a inu a boma?Ayi zikomo mukhale ndi moyo opanda malire inu ndi anzeru anuwo oweruza mosaopa Mulungunu.

Comments are closed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading