National

Khoti likhululukila mwana wa nduna okuba galimoto

By Kondwani Mkhalipi-Manyungwa

January 26, 2018

Zina ukamva kamba anga mwala ndithu. Pamene okuba mbuzi akutsekeledwa zaka, okuba galimoto akuchoka ku Khoti akusekelela.

Bwalo la majisitileti ku Blantyre lagamula amuna awiri amene anaba galimoto kuti atsatsekeledwe. Ati m’malo mwake asachimwenso basi.

Awiriwo ndi mwana wa mkulu wa bizinesi a Mike Mlombwa ndi mwana wa nduna yakale a Bazuka Mhango. Onse awiriwa ali ndi mayina onga atate awo, amangoonjezelako Junior basi.

Bwalo linauzidwa kuti awiriwa anaba galimoto ya Nissan Tiida ku malo a chisangalalo a Dusk mu boma la Blantyre.

Iwo ati ataba galimotoyo anapezamo zinthu zimene anazigulitsa. Zithunzo anali ma foni a m’manja atatu ndi kompyuta yoyenda nayo, laputopu.

Iwo ati kenako anayamba kufufuza msika wa galimoto limene anabalo. Ati cholinga chawo chinali choti akagulitse zida za galimotolo.

Apolisi ananyengezela kuti ndiwo akufuna kugula galimotolo ndipo awiriwa atalibweletsa ananjatwa ndi kutengeledwa ku bwalo.

Atafika ku bwalo, ogamula anawapeza olakwa ndipo m’malo mowatumiza ku ndende iye anachita za Yesu zowamasula ndi kuwauza asakachimwenso.

Izi zakhumudwitsa a Malawi angapo.