Khoti likhululukila mwana wa nduna okuba galimoto

Advertisement
Court

Zina ukamva kamba anga mwala ndithu. Pamene okuba mbuzi akutsekeledwa zaka, okuba galimoto akuchoka ku Khoti akusekelela.

Bwalo la majisitileti ku Blantyre lagamula amuna awiri amene anaba galimoto kuti atsatsekeledwe. Ati m’malo mwake asachimwenso basi.

CourtAwiriwo ndi mwana wa mkulu wa bizinesi a Mike Mlombwa ndi mwana wa nduna yakale a Bazuka Mhango. Onse awiriwa ali ndi mayina onga atate awo, amangoonjezelako Junior basi.

Bwalo linauzidwa kuti awiriwa anaba galimoto ya Nissan Tiida ku malo a chisangalalo a Dusk mu boma la Blantyre.

Iwo ati ataba galimotoyo anapezamo zinthu zimene anazigulitsa. Zithunzo anali ma foni a m’manja atatu ndi kompyuta yoyenda nayo, laputopu.

Iwo ati kenako anayamba kufufuza msika wa galimoto limene anabalo. Ati cholinga chawo chinali choti akagulitse zida za galimotolo.

Apolisi ananyengezela kuti ndiwo akufuna kugula galimotolo ndipo awiriwa atalibweletsa ananjatwa ndi kutengeledwa ku bwalo.

Atafika ku bwalo, ogamula anawapeza olakwa ndipo m’malo mowatumiza ku ndende iye anachita za Yesu zowamasula ndi kuwauza asakachimwenso.

Izi zakhumudwitsa a Malawi angapo.

Advertisement

64 Comments

 1. Amabungwe Ali Ziiii Osanenapo Kanthu Alandila Mamanja Anthu Oyipa Inu Nkhani Ya Cash get Mukulephela Kumugwila Joice Banda Bakili Angonjoya , Chaponda Angonjoya Anthu Okuba Inu Lero Mwatibwelesela Chiphaso Mukuti Tizilipira Pachaka Muzakhutisidwa Liti? Bolaso Ku Iguputo Kokuja

 2. Apa sizinayende bwino. Chilungamo palibe. Ndiye chifukwa chache anthu akagwira wakuba amangopheratu. Amaopa nyansi ngati izi. Kuli anthu ambili ku chichi, maula ndi ndende zina omwe mwina anaba half bag ya chimanga nkugwidwa. Awa anawa amayenera akasewenze ku ndende. Ngati sapita ku ndende pakhala povuta kuti ma khoti atumize ankuba ena ku ndende pomwe akuba ena akhululukidwa. Kodi judge ameneyu sukulu anakaphunzila kuti?

 3. Ifvyou can’t beat them join them; nkhani apa pangani ndalama and you will join the elite! Osamangoti God will intervene this that while anzanu ndalama is intervening! Inu ntchito kumati ndadya bebi yakuti yakuti! Mumva painz

 4. Judge walandira zingati? Chilungamo palibepo apa. A police akugwira ntchito modzipereka ndipo akupangidwa ulesi ndi oweluza milandu makape amenewa. Thandizani okubawo apolisi akamubere yake galimoto judge ameneyo ndi opusa

 5. Asiyeni adzikondera choncho koma court lakumwamba, ndilomwe lidzagamule milandu ya winaaliyense mwachilungamo. Dziko, limakondera koma boma lakumwamba, sipadzakhala zimenezo osauka alibe mphamvu yowapulumutsa m’manja mwaoweruza achinyengo.

 6. I always say our judges and magistrates are very corrupt,this is a simple example,,corruption at its best.By the way what’s the name of the magistrate.

 7. Ali mayiko ena, the state could have appealed the judgement. This is very unfair to those who are in prison or have been there for stealing a stainless razor blade.

 8. Ali mayiko ena, the state could have appealed the judgement. Paja Mlombwa snr anagula fridge K4 million pa Blue night fundraising chaka chinacho.

 9. Muthu Olezela Ofuna Kulandila Envilop Kwapulent Kundende Pomwe Uyu Zokoza Kuba Galimoto Kumutaya Aaa Malawi Choona Chili Pati?

 10. kma chavura. mukumusunga ku police jst bcz of song. mbava kukhululukiridwa shame on u, akukanthani mulungu n ma drought avutawa it’s because of ur injustice n immorality

 11. Uku ndiye kulimbikitsa umbava ndi umbanda chifukwa mosazindikira kanthu mwina sakudziwa kuti zija tikuwona zomatsomphora apresident envelope zija zifukwa zina ndi momwe akuchita amakhoti akamapeleka zigamulo zosakhala bwino ngati izi Chonchi palibe angasiye mchitidwe wokuba

 12. Wins kupanga compose nyimbo akukanika kumpasa bail,wokuba zinthu zama million osatsekeledwa kundende,Malawi wanga ukupita kuti nanuso amabungwe simmatithandiza you are just sitting and seeing.Malawi is full of corruption. Shithole country as Trump said.

 13. Yemwe walamula kuti mlandu watha iyeso ndiwakuba.kukhala Mwana wanga kumulamura dzaka dzisanu,koma poti ndimwana wamuthu ochita bwino ndichifukwa waturuka.Komaso Athu akamati kunja kuno kuli Mankhwala mukhulupilire,palikathu.And ineyo ndimakhulupirila kuti pali makhwara amatulusa muthu roko atapha muthu dzake amatuluka.

 14. chavura sanabe kathu kapena kuononga pena pake koma akutsekelabe mpaka pano wina kuba galimoto akut amukhulukila hahaha

 15. Nchifukwa chake ndimadana ndi kusauka. Ukakhala osauka ndithu ukhoza kuuzidwa ukolope mu chimbuzi ndi Lilime.chifukwa chofuna ndalama kukolopa ndithu nanga upanga bwanji?

Comments are closed.