K3000 yokha itha kupulumutsa otsomphola Mutharika

33

Bambo Francis Itende amene anatsomphola phasulo la a Mutharika agamulidwa kuti ndi olakwa.

A Itende amene anachita chipongwe chawo chaka chatha pa 23 December anatsomphola phasulo m’manja mwa a Mutharika ati chifukwa amayesa muli ndalama.

Izi zinachitika m’boma la Zomba, pa Songani pamene a Mutharika anaima kuti agawe ndalama kwa amayi amene amawavinila pa msonkhano.

A Itende amaimbidwa mlandu ofuna kudzetsa chisokonezo.

Pa mlanduwu iwo apezeka olakwa ndipo oweluza wati chigamulo apeleka lachisanu pa 19.

Mlandu ofuna kudzetsa chisokonezo chilango chake ndi choti munthu amatha kutsekeledwa kwa theka la chaka (miyezi isanu ndi umodzi) kapena kulipila chindapusa cha K3000 basi.

Share.

33 Comments

  1. My question is where were those who provides security to him, apatu ndiye kuti the security is lapse anawabondetsa,koma akamayenda ngati zeni zeni they are just figure heads and needs overhaul

  2. Limenelo ndiye dziko mwana wanga tsala uzione mpaka President kulimba mtima kumakamba nkhani against munthu ovetsa chisoni chonchi mpakana kulola akalowe mndende osangomukhulukira bwanji monga baibulo limanenera tiyeni timuziwe Yesu a Malawi a Munthalika ndiolimba mtima akanakhala Muluzi sizikanafika APA amaziwa zosowa za a Malawi

  3. Ayi tiyeni apa tikhale ndi umunthu mwina pa mbiri ya Malawi palibe munthu analimba mtima mpakana kufika apa. Muganize mozama mmene pamakhalira pa malo a President ndani angalimbe mtima nkupanga izi. So mwina munthuyu anavutika kwambiri so kunali kupempha mwachikulu. Tangoganizani mmene security ya a President imakhalira muja ndani angalimbe mtima kufuna kumubera President sangathe kuthawa. Munthu uyu amafuna atawapempha a President kuti ndavutika ine. Onaninso kupita ku khothi aaaaa inu akudziwa munthuyu inali njira yopempnera angomupatsa fine ya K3000 basi.

  4. hahaha i see no issue here..mbava zili mmanyumba mwawo mu 47 ka mwana kanjala ngati aka kukalanga..!!Achina chaponda,Joyce banda e.t.c ali kuti the deserve this punishment.. kutsophola president is a sign kuti ndalama ikusowaa

  5. Ngati pali amene akumuziwa munthuyo plz contact me on +27603338801/+2782443905 mukhoza kundipezanso pa whatsapp both number… Yesesani guyz I promise I’ll pay for him 3000 is not a big deal

  6. Eish dziko lapasi zovuta amphawi ena akuba ma Billion mpaka pano milandu yao sinalo ndimu court komwe….wina wangotsophola achitetezo ali pomwepo dzulo mulandu wagamulidwa kale.ambuye bwelani ndithu.

  7. kachapa –uzlbe mzeru nkhani ndyot anatsophola nt if de president was killd dats anothr issue nkhani yapa court ckambdwa mmafanizo let the 3000 free him up***bola anadzwa kt amalawi akufuna ndalama n kulibe chtetezo cha president ku nyasaland its izy to kill him