Pulofeti amangidwa kamba ka ulosi wa bodza

Advertisement
CUFF

Tsopano mukakhala mmaluzi ndi kuganiza zoyamba bizimisi ya Tchalitchi muli muzichita uneneri, musamale. Azikumangani.

A Polisi ku Thyolo anjata ndi kutengela ku Khoti Bambo Sampulo Newiri a utumiki otchedwa Thamanda ati kamba kofalitsa uthenga wa bodza ndi osokoneza anthu.

MachingaMalinga ndi a Polisi, Bambo Newiri amene ali ndi zaka 40 akumachita utumiki wawo ku Thyolo umene ukupomboneza anthu.

Mwa zina, a Newiri amauza anthu owatsatila kuti asamatumize ana awo ku sukulu ndinso kuti akadwala asapite ku chipatala.

A Newiri anauzanso owatsatila kuti asalime minda yawo chaka chatha ati chifukwa Ambuye anawaonetsa kuti mvula siyigwa konse. Anthu anamvela ndipo ngakhale Mvula inabwela, iwo anali manja pindike. Owatsatilawo ati tsopano akukhalila kupempha kwa anthu.

Anthu a ku Thyolo ndiwo adakamang’ala ku Polisi kuti ziphunzitso ndi uneneri wa a Newiri ukusokoneza chitukuko ku dera lawo. Apolisi anapita ndi kunjata a Newiri. Ndipo adawatengela ku bwalo la Milandu.

Pa bwalo la Milandu, a Newiri aukana mlandu ofuna kudzetsa chisokonezo ndi zokamba zawo. Apolisi anapempha a bwalo kuti awalole kubweletsa mboni. Ndipo a bwalo anena kuti mboni zitatu zibwele pa 22 mwezi uno.

Otsatila a Newiri amene anawatsatila ku Khoti atavala zovala zoyela zokhazokha ananena kuti milandu yomwe akuzengedwa Mtsogoleri wawo ndi ntchito za Satana.