Anjatwa kamba kotsomphola Mutharika

Advertisement
Machinga

Patsepatse nkulanda. Kupalamula ndi konse ndithu koma milandu inayi ndendende kugenda ku Polisi wamkulu fodya ali mthumba.

Bambo wina wa zaka makumi awiri ndi mphambu zisanu kudza imodzi (26) ali m’manja mwa a Polisi atagwidwa pamene amafuna kutsomphola phasulo m’manja mwa Mtsogoleri wa dziko lino a Peter Mutharika.

MachingaA Bambo Francis Itende ati anachita chipongwe chawochi pa 23 December chaka chatha pa Songani mu boma la Zomba.

Ati a Mutharika anayima pa malowa kuti agawile kangachepe kwa amayi a chipani chawo cha DPP amene amawayimbila nyimbo.

Apa Bambo Itende anaonapo mwayi oti atsanzikane ndi umphawi.

Ndiye pamene a Mutharika amafika, iwo basi tsompho! kulanda phasulo lomwe a Mutharika adanyamula.

Iwo sanapite patali ndi upandu wawo ndipo a chitetezo cha a Mutharika adawambwandila.

A Itende amene amachokela ku Dedza akuyembekezeka kukalowa mu Khoti.

Advertisement

61 Comments

 1. Naye Gwaladi anyanya kugawa makobili.Don’t he know kt this is Tantamount to February??? Ma envelope mbwe ngat amagwila ganyu Post Offece.Anafunaka mukumulanda evelopyo nd kumutibulaso Makofi athazi angazaname

 2. Koma Peter Ndi chitsilu cause munthu amafuna kumupatsa ulemu kumunamizira kut akufuna kumubera 2019 peter usawuka coz mitsokho sutegaso ufalika chitsilu

 3. Kkkkk ameneyo Ali gulu LA anthu amene amatizunguza kupulaimale ndithu kkkk mpaka wakatsompholaso President kkkk achitetezo anali kokamwa matokoso eit?kkkk

 4. Chonde mwanayo musamupange tintini ndiwosalakwa vuto ndi achitetezo alephela ntchito yawo.apresdent pamenepo adziwe kuti alibe security kodi pamenepa mwanayo akanakhala kuti anatenga bomba sibasi apatu gwape anafatu.

 5. Where was body guards? And why are you publishing this because you are jeopardising president security. Bodyguards need more training of escorting VIP. This is embarrassment. Why did they give home a chance to come close? Eish koma Malawi

 6. Mmm gyz ine ndnalipopo, nkhan ndyoti adawa analezela ndye amafuna kumugwra zanja presedent pamene amaweva mfanz. By dat tym mmanja mwa peter mudalibem kath.

 7. Ine zakubazo ayi, koma ndati ndi gonenako pa amene mumakhala busy kumachonga zomwe anzanu alemba. Nthawi zina ndibwino kukhala chete ngati ulibe zonena. Meachitsanzo; ena mukuseka mau akuti anjatwa, ine ndikutsimikizireni kuti amene walemba mau awa ku school adapitako. Ndipo school yake yaukachenjede. Ambiri timalimba chichewa kapena chingerezi cholakwika. Kwa amene akuona ngati liwu lakuti anjatwa ndilolakwika, ameneyo alitenso nkalasi ya Chichewa ndipo akaphunzire phunziro la mau onyazitsa. Kumeneko akapeza mau ngati amenewa, kungoonjezapo akapezaso mau ngati pezwa, mangwa, pangwa, menywa, etc. Ndiye chonde tiyeni tizingowerenga ndikunva chomwe chikukambidwa kusiyana ndikumakhalira kuchonga zolemba ena. What one doesn’t know doesn’t exist. Ndangodutsa

 8. amafuna kumudziwitsa peter kut chitetezo mulibe mdziko muno komanso maluzi avuta kwambiri.nanga ngat akubeledwa mtsogoleri wa dziko kulibwanji nzika za mdzikomo.am not from mcp or pp but am a citizen of the republic of MALAWI.

 9. Next time tizanva kut amuba, nanga security yake imene ija munthu nkusomphola ndala mmanja ma president alinso mgalimoto?? Haha ndikanakhal ine ndikapanga za sacking bas alephela pa ntchito yao ya chitetezo.

 10. Vuto losekerera ma Cadet ndi limenelo. Ngati mumawasekerera kuti azimenya a police as they did pa Tsangano. Here it is now. They don’t fear even the State President security. Mwana wokulira pa chilolo…………. Musamulange ndi wanu mudamuzoloweza kale. Vuto si iyeyo, mixxx

 11. kumanga munthu osalakwa pomwe MUTHALIKAYO tsiku ndi tsiku akuba misonkho ya amalawi? kumeneku ndikulakwa.MOTI M’LANDU WA CHAPONDA NDI UWUWU waukulu ndi ut?

  1. Iyayi, sigalu, nanga si akudabwa kuti inu Chichewachi mwachidabwa, misintho ya aneni simukuyidziwa inu, nchifukwa akukunenani ka, kapena akanati Angerezi inu?! Adm, walemba zomveka kwambiri, 2pts… Mmmmmh.

Comments are closed.